Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chifuniro cha Mulungu N’chotani?

Kodi Chifuniro cha Mulungu N’chotani?

Mulungu akufuna kuti tidzakhale mwamtendere komanso mosangalala m’paradaiso padziko lapansi pano kwamuyaya.

Koma mwina mungafunse kuti, ‘Kodi zimenezi zingatheke bwanji?’ Baibulo limanena kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene udzachite zimenezi, ndipo Mulungu akufuna kuti anthu onse adziwe za Ufumu umenewu ndiponso zimene iye akufuna kuwachitira.​—Salimo 37:11, 29; Yesaya 9:7.

Mulungu akufuna kuti zinthu zizitiyendera bwino.

Mofanana ndi bambo wachikondi amene amafuna kuti ana ake zinthu ziziwayendera bwino, Atate wathu wakumwamba akufuna kuti tikhale osangalala panopa mpaka muyaya. (Yesaya 48:17, 18) Iye analonjeza kuti “wochita chifuniro cha Mulungu adzakhala kosatha.”​—1 Yohane 2:17.

Mulungu akufuna kuti tiziyenda m’njira zake.

Baibulo limanena kuti Mlengi wathu akufuna ‘kutiphunzitsa njira zake’ n’cholinga choti ‘tiziyenda m’njira zakezo.’ (Yesaya 2:2, 3) Iye wasonkhanitsa “anthu odziwika ndi dzina lake” kuti athandize anthu onse kudziwa chifuniro chake padziko lonse lapansi.​—Machitidwe 15:14.

Mulungu akufuna kuti tonse tizimulambira mogwirizana.

Kulambira Yehova m’njira yovomerezeka, sikumagawanitsa anthu koma kumawagwirizanitsa, chifukwa amasonyezana chikondi chenicheni. ( Yohane 13:35) Kodi ndani masiku ano amene akuphunzitsa amuna ndi akazi kulikonse kuti azitumikira Mulungu mogwirizana? Kuti mupeze yankho la funso limeneli, tikukupemphani kuti mupitirize kuphunzira kabuku kano.