Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Zosankha Zomwe Zimasonyeza Kuti Timadalira Yehova

Zosankha Zomwe Zimasonyeza Kuti Timadalira Yehova

Tsiku lililonse, timafunika kusankha zinthu zosiyanasiyana. Nthawi zambiri anthu m’dzikoli amasankha zinthu potengera mmene akumvera mumtima kapena amangotsanzira zimene anthu ambiri amachita. (Eks 23:2; Miy 28:26) Koma mosiyana ndi zimenezi, anthu amene amadalira Yehova ‘amamukumbukira’ mwa kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo kuti ziziwatsogolera akamasankha zochita.​—Miy 3:5, 6.

Pa lemba lililonse m’munsimu, lembani nkhani yosonyeza mmene lembalo lingakuthandizireni posankha zinthu mwanzeru.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZITSANZIRA ANTHU A CHIKHULUPIRIRO, OSATI OPANDA CHIKHULUPIRIRO​—MOSE, OSATI FARAO, KENAKO YANKHANI FUNSO LOTSATIRALI:

Kodi chitsanzo cha m’Baibulo chinathandiza bwanji m’bale wa muvidiyoyi kuti asankhe zinthu moyenera?