Onani zimene zilipo

Kodi Mboni za Yehova Zili ndi Abusa Amene Amalipilidwa?

Kodi Mboni za Yehova Zili ndi Abusa Amene Amalipilidwa?

Monga mmene zinalili mumpingo wacikristu wa m’nthawi ya atumwi, m’gulu la Mboni za Yehova mulibe anthu amene amaonedwa kuti ndi apadela. Abale ndi alongo onse mumpingo ndi atumiki oikidwa ndipo amagwila nchito yolalikila ndi kuphunzitsa anthu mau a Mulungu. Mumpingo uliwonse muli abale ndi alongo pafupifupi 100. Mumipingo imeneyi muli amuna okwima mwakuuzimu amene amatumikila monga “akulu.” (Tito 1:5) Akulu amenewa amagwila nchito imeneyi popanda malipilo.