Onani zimene zilipo

Kodi Ndalama Zoyendetsela Nchito ya Mboni za Yehova Zimacokela Kuti?

Kodi Ndalama Zoyendetsela Nchito ya Mboni za Yehova Zimacokela Kuti?

Ndalama zimene timayendetsela nchito yathu yolalikila zimacokela makamaka kwa Mboni za Yehova zimene zimapeleka mwa kufuna kwao. Ndipo pa misonkhano yathu sipayendetsedwa mbale ya zopeleka ndiponso sitipeleka cakhumi. (Mateyu 10:7, 8) Koma pa misonkhano yathu pamakhala mabokosi a zopeleka kuti aliyense amene afuna aponyemo ndalama. Ndipo sitilengeza maina a anthu amene aponyamo.

Ndalama zimenezi zimakwanila kuyendetsela nchito yathu cifukwa cakuti tilibe abusa amene amalipilidwa. Cinanso n’cakuti Mboni za Yehova sizipatsidwa ndalama pa nchito yao yolalikila komanso nyumba zathu zolambilila si zapamwamba kwambili.

Ndalama zikatumizidwa ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova amazigwilitsila nchito kuthandiza anthu amene akhudzidwa ndi ngozi zacilengedwe, ndi kusamalila amishonale, ndiponso atumiki oyendela mipingo. Ndalama zina zimathandiza pa nchito yomanga nyumba zolambilila, ndiponso pa nchito yosindikiza ndi kutumiza Mabaibulo ndi mabuku ena.

Munthu aliyense angasankhe kupeleka ndalama zothandizila pampingo kapena pa nchito yathu ya padziko lonse kapenanso pa zonse ziŵili. Mwezi uliwonse mpingo umadziŵitsa anthu a mumpingomo za mmene ndalama zayendela mwezi umenewo.