Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Ana a sukulu akuphunzila m’kalasi ya Sukulu ya Giliyadi ya mu 2017

MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO

Sukulu ya Giliyadi—Ophunzila Ake Amacokela Padziko Lonse

Sukulu ya Giliyadi—Ophunzila Ake Amacokela Padziko Lonse

DECEMBER 1, 2020

 Caka ciliconse, atumiki ena a nthawi zonse apadela ocokela padziko lonse lapansi amaitanidwa kuti akaloŵe Sukulu Yophunzitsa Baibo ya Giliyadi, imene imacitikila ku Patterson, mumzinda wa New York. a M’sukulu imeneyi, ophunzila amaphunzitsidwa mmene angacitile bwino mautumiki awo osiyana-siyana m’gulu la Yehova. Maphunzilo amene amalandila amawathandiza kulimbitsa mipingo na maofesi a nthambi padziko lonse lapansi.

 Kukamba zoona, Sukulu ya Giliyadi ni ya padziko lonse. Mwacitsanzo, kalasi ya namba 147 imene inacitika mu 2019, inali na ophunzila 56 ocokela m’maiko 29. Akhristu amene amaloŵa Sukulu ya Giliyadi ni atumiki a nthawi zonse apadela amene akhala akutumikila monga atumiki a pa Beteli, atumiki a madela, amishonale, kapena apainiya apadela.

 Nchito yokonzekela maphunzilo a sukuluyi imayamba kukali nthawi yaitali. Dipatimenti ya ku Likulu Yoona za Mayendedwe imagulila abale na alongo okaloŵa sukuluyi matiketi a ndeke. Mwacitsanzo, pa kalasi ya 147 ya Giliyadi, wophunzila aliyense wocokela ku dziko lina kupita ku Patterson, pa avaleji anaseŵenzetsa ndalama zokwana madola 1,075 a ku America, kupita na kubwela. Ophunzila a ku Solomon Islands anayenda maulendo anayi a pandeke kuti akafike ku Patterson, komanso maulendo atatu a pandeke kuti abwelele kwawo. Tikaphatikiza pamodzi, iwo anayenda mtunda wa makilomita 35,400! Maulendo amenewo anawononga ndalama zokwana madola 2,300 a ku America pa wophunzila aliyense. Pofuna kucepetsako ndalama zowonongeka, Dipatimenti Yoona za Mayendedwe ku Likulu imaseŵenzetsa pulogilamu ya pa kompyuta pofufuza mitengo ya maulendo a pandeke kuti ipeze mitengo yochipilako. Ngakhale pambuyo popeza tiketi ya mtengo wabwinopo, pulogilamu ya pakompyuta imeneyo imapitilizabe kusakila kwa mawiki ngakhale kwa miyezi, kuti ione ngati mitengo yatsikako. Dipatimenti ya Mayendedwe imeneyi imaseŵenzetsanso mabonasi a maulendo a pandeke, amene anthu amacita copeleka.

 Ophunzila ambili amafunikila ciphaso coloŵela m’dziko la United States. Dipatimenti ya Zamalamulo ya ku Likulu ndiyo imawathandiza kupeza ziphaso zimenezi. Pa avaleji, ndalama yolembetsela na kugulila ciphaso coloŵela m’dziko ca wophunzila mmodzi, inali madola 510 a ku America.

 Kodi timapindula bwanji na maphunzilo amene oloŵa Sukulu ya Giliyadi amalandila? M’bale Hendra Gunawan ni mkulu mumpingo m’dziko lina kum’mwela ca kum’maŵa kwa Asia. Mumpingo mwawo muli banja limene linatsiliza maphunzilo a Giliyadi. Iye anati: “Poyamba, mumpingo mwathu munalibe apainiya a nthawi zonse. Koma banja lotsiliza maphunzilo a Giliyadi limeneli litafika, ena mumpingo analimbikitsidwa na mtima wawo wokangalika komanso wodzipeleka potumikila, cakuti anayamba kucita upainiya. M’kupita kwa nthawi, mlongo wina mumpingo mwathu anafika ngakhale poloŵa Sukulu ya Alengezi a Ufumu!”

 M’bale Sergio Panjaitan, amene amatumikila pa ofesi ina ya nthambi kum’mwela ca kum’maŵa kwa Asia amaseŵenzela pamodzi na atumiki otsiliza maphunzilo a Giliyadi. Iye anati: “Maphunzilo amene iwo analandila ni dalitso kwa iwo komanso kwa ife. Iwo anaphunzila zambili! Koma sadzionetsela na zimene anaphunzila. M’malomwake, amauzako ena zimene anaphunzilazo. Izi zimatilimbikitsa, ndipo nafenso timalimbikitsako ena.”

 Kodi ndalama zoyendetsela sukuluyi zimacokela kuti? Zimacokela pa zopeleka za nchito ya padziko lonse, ndipo zambili zimapelekedwa potsatila njila zimene zili pa donate.isa4310.com. Zikomo kwambili cifukwa ca zopeleka zanu zimene mumapeleka mowoloŵa manja. Zopelekazi zimathandiza poyendetsa Sukulu ya Giliyadi, imene ophunzila ake amacokela padziko lonse.

a Maphunzilo a sukuluyi amakonzedwa na Dipatimenti ya Maphunzilo a Zaumulungu, imene imayang’anilidwa na Komiti Yoyang’anila Nchito Yophunzitsa ya Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova. Amene amaphunzitsa sukuluyi ni alangizi ocokela m’Dipatimenti ya Maphunzilo a Zaumulungu komanso alangizi ena, kuphatikizapo abale a m’Bungwe Lolamulila.