Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Pokonza seŵelo la m’Baibo limeneli, tinagula miyala yopela-pela yolemela makilogilamu oposa 27,500 n’kuibweletsa mu situdiyo ya Mt. Ebo

MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO

Kupanga Mavidiyo a Msonkhano Wacigawo wa mu 2020 Wakuti ‘Kondwelani Nthawi Zonse’!

Kupanga Mavidiyo a Msonkhano Wacigawo wa mu 2020 Wakuti ‘Kondwelani Nthawi Zonse’!

AUGUST 10, 2020

 Mavidiyo a msonkhano wacigawo amatifika pamtima na kutithandiza kumvetsetsa zimene Baibo imaphunzitsa. Msonkhano Wacigawo wa mu 2020 wakuti ‘Kondwelani Nthawi Zonse’! unali na mavidiyo 114 na nkhani 43 zokambidwa na a m’Bungwe Lolamulila komanso abale owathandiza. Kodi munaganizilapo za kukula kwa nchito imene imacitika ndiponso kuculuka kwa ndalama zimene zimagwilitsidwa nchito popanga mavidiyo amenewa?

 Abale na alongo pafupi-fupi 900 padziko lonse anagwilitsa nchito nthawi na maluso awo pothandiza kuti pulogilamuyi itulutsidwe. Pogwila nchitoyi, onse pamodzi anataila maola pafupi-fupi 100,000 m’zaka zoposa ziŵili. Maola amenewa aphatikizapo maola 70,000 amene anagwilitsidwa nchito pokonza seŵelo la m’Baibo la mphindi 76 lakuti, Nehemiya: “Cimwemwe Cimene Yehova Amapeleka Ndico Malo Anu Acitetezo.”

 Kuti nchitoyi itheke, panafunika ndalama zambili zosamalila anchito odzipelekawa, kugulila zipangizo na zinthu zina zofunikila.

 M’bale Jared Gossman wa m’Dipatimenti Yoona za Mavidiyo na Zomvetsela, anati: “Komiti Yoyang’anila Nchito Yophunzitsa ya Bungwe Lolamulila imafunitsitsa kuti abale na alongo a zikhalidwe komanso a m’madela osiyana-siyana azipezeka m’mavidiyo athu. Izi zimathandiza kuonetsa kuti ndifedi gulu la abale la padziko lonse. Kuti zimenezi zitheke, magulu 24 a m’maiko 11 anaseŵenzela pamodzi pogwila nchitoyi. Pamafunika ndalama zambili, kulinganiza bwino zinthu, komanso kucita zinthu mogwilizana kuti anthu a m’maiko osiyana-siyana aseŵenzele pamodzi.”

 Mavidiyo athu ambili amafuna zipangizo zapadela na malo apadela ojambulila. Mwacitsanzo, popanga Seŵelo lakuti Nehemiya: “Cimwemwe Cimene Yehova Amapeleka Ndico Malo Anu Acitetezo,” anakonza bwalo lapadela lojambulila mu situdiyo ya Mt. Ebo kufupi na ku Patterson, New York, ku America. Abale anafuna kuti m’seŵeloli muzionekabe zinthu zacikale-kale koma asawononge ndalama zambili za gulu. Kuti izi zitheke, anamanga mpanda wamatabwa na kuupenta kuti uzioneka ngati mpanda wa Yerusalemu wakale. Cigawo ciliconse ca mpandawo cinali cacitali mamita 6, ndipo anacipenta kuti cizioneka monga cipupa camiyala. “Zipupa” zimenezo anazikonza m’njila yakuti azikwanitsa kuzinyamula n’kuziika pamalo ena pojambula mbali ina ya seŵelo. Izi zinathandiza kuti pasafunike zinthu zambili zokonzela bwalo lojambulila. Ngakhale n’conco, tinawononga ndalama pafupi-fupi madola 100,000 a ku America pokonza cabe bwalo lojambulila seŵeloli. a

 Kudziŵa zonse zimenezi kumatithandiza kuyamikila kwambili pulogilamu ya msonkhano wacigawo wa caka cino. Tili na cikhulupililo cakuti khama limene tinaonetsa potulutsa pulogilamu imeneyi linathandiza kuti Yehova atamandidwe padziko lonse. Tiyamikila zopeleka zimene munapeleka mooloŵa manja pocilikiza nchito ya padziko lonse kupitila pa donate.isa4310.com komanso mwa njila zina.

a Bwalo loseŵenzetsa popanga Seŵelo lakuti Nehemiya: “Cimwemwe Cimene Yehova Amapeleka Ndico Malo Anu Acitetezo” linakonzedwa mlili wa COVID-19 usanayambe. Panthawiyo, sipanali kufunika kukhala motalikilana.