Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO

Kabokosi Kakang’ono Kopelekela Cakudya Cauzimu

Kabokosi Kakang’ono Kopelekela Cakudya Cauzimu

SEPTEMBER 1, 2020

 Masiku ano, Mboni za Yehova zimalandila cakudya cauzimu cambili kupitila pa zipangizo kuposa kale lonse. Koma m’madela ambili padzikoli, abale sakwanitsa kulumikiza ku intaneti. Ena amakhala m’madela amene netiweki imaduka-duka, ni yocepa mphamvu, kapena kulibiletu netiweki.

 Ngakhale n’telo, abale na alongo athu ambili masiku ano amakwanitsa kucita daunilodi zofalitsa za pacipangizo popanda kulumikiza ku intaneti. Kodi amakwanitsa bwanji?

 Ofesi ya nthambi imatumiza tumabokosi tung’ono-tung’ono tochedwa JW Box ku mipingo ya ku madela amene intaneti ni yovuta. Kabokosi kalikonse kali na kacipangizo kokhala na netiweki yake-yake kamene kanagulidwa ku kampani inayake. Kamagwila nchito potsatila pulogilamu ya pa kompyuta yopangidwa na Dipatimenti ya Makompyuta ku Beteli. Komanso kamakhala na zofalitsa za pacipangizo na mavidiyo a pa jw.org. Kabokosi kamodzi amakagulitsa madola 75 a ku America.

 Pa Nyumba ya Ufumu, abale na alongo amalumikiza mafoni na matabuleti awo ku ka JW Box na kucita daunilodi zofalitsa na mavidiyo. Ngakhale amene ali na mafoni akale kapena ochipa angalumikize. Koma bwanji ngati kumene kuli mpingo kulibe intaneti? Kodi umakwanitsa bwanji kukhala na zofalitsa zatsopano mu JW Box? Nthawi na nthawi ofesi ya nthambi imatumiza mafulashi okhala na zofalitsa zatsopano za pa jw.org zimene mpingo ungacite daunilodi pa JW Box. Fulashi iliyonse imagulidwa madola anayi a ku America.

 Kodi JW Box yathandiza bwanji abale athu? M’bale Nathan Adruandra wa ku Democratic Republic of Congo amene ni kholo anati: “Kwa nthawi yaitali nakhala nikuyesa kucita daunilodi maseŵelo akuti, ‘Mulungu Wanga, Cikhulupililo Canga Cili mwa Inu’ na Kumbukilani Mkazi wa Loti. Koma sin’nakwanitse ndipo izi zinali kunilefula. Tsopano n’nakwanitsa kucita daunilodi mavidiyo amenewa ndipo izi zatithandiza ife makolo kuphunzitsa bwino ana athu.”

 M’bale amene amathandiza mipingo kuseting’a ka JW Box ku Nigeria anati: “Abale amaona kuti JW Box ni mphatso yapadela yocokela kwa Yehova. Iwo ni okondwela kuti tsopano amacita daunilodi mosavuta zofalitsa na mavidiyo a m’Thuboksi yathu yophunzitsila.”

 Ma JW Box oposa 1,700 atumizidwa kale kwa abale athu mu Africa, ku Oceania, komanso ku South America ndipo makonzedwe ali mkati otumiza mabokosi amenewa ku mipingo inanso yambili. Kodi ndalama zogulila ma JW Box amenewa zimacokela kuti? Zimacokela pa zopeleka za padziko lonse zimene ambili amapeleka kupitila pa donate.isa4310.com. Zikomo kwambili cifukwa cocilikiza moolowa manja.