Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MMENE ZOPELEKA ZANU ZIMAGWILILA NCHITO

Cikondi Capaubale Cinaonekela pa Nchito Yopeleka Thandizo mu 2022

Cikondi Capaubale Cinaonekela pa Nchito Yopeleka Thandizo mu 2022

JANUARY 1, 2023

 Baibo inakambilatu kuti m’masiku athu ano, kudzakhala nkhondo, zivomezi, milili, komanso kudzaoneka zoopsa zina. (Luka 21:10, 11) Mawu aulosi amenewa anapitilizabe kukwanilitsidwa m’caka ca utumiki ca 2022. a Mwacitsanzo, nkhondo ya ku Ukraine inapitilizabe ndipo inakhudza miyoyo ya anthu mamiliyoni ambili. Ndipo m’maiko ambili mlili wa COVID-19 unali usanatheletu. Kuwonjezela apo, anthu osaŵelengeka anakhudzidwa na masoka a cilengedwe monga zivomezi ku Haiti, komanso mvula yamkuntho yowononga ku Central America ku Philippines na kummwela ca kum’mawa kwa Africa. Kodi Mboni za Yehova zinawathandiza bwanji anthu okhudzidwawo?

 M’caka cautumiki ca 2022, gulu lathu linapeleka thandizo kwa anthu pamatsoka pafupifupi 200. Ndalama zonse pamodzi zimene tinagwilitsa nchito popeleka thandizo, zinakwana madola pafupifupi 12 miliyoni. b Onani mmene zopeleka zinagwilila nchito pothandiza anthu amene anakhudzidwa na matsoka aŵili otsatilawa.

Zivomezi ku Haiti

 Pa August 14, 2021, civomezi ca mphamvu kwambili cinagwedeza kummwela kwa dziko la Haiti. N’zacisoni kuti Mboni zitatu zinafa. Anthu amene anapulumuka civomezico anavutikabe cifukwa zinthu zawo zinawonongeka, anavulazika komanso anavutika na cisoni cifukwa cotaikilidwa okondedwa awo. M’bale wina dzina lake Stephane anati: “Mumzinda wonse munafa anthu ambili moti panali kucitika malilo ambili ndithu mlungu uliwonse kwa miyezi yoposa iŵili.” M’bale winanso dzina lake Éliézer,anati: “A Mboni ambili analibe pogona, zovala, nsapato na zinthu zina zofunika pa umoyo. Kwa miyezi, anthu ambili anali na mantha cifukwa camgwedegwede umene unali kucitika pambuyo pa civomezi.”

 Gulu lathu linapeleka thandizo mwamsanga. Ofesi ya nthambi ku Haiti inapeleka cakudya coposa matani 53, matenti, mamatilesi, komanso machaja a foni ogwilitsila nchito sola. Kuwonjezela apo, m’caka cautumiki ca 2022, nyumba zoposa 100 zinamangidwanso kapena kukonzedwa. Tinaseŵenzetsa ndalama zoposa madola 1 miliyoni popeleka thandizo limeneli.

Kupeleka zakudya ku Haiti

 Abale na alongo athu ni oyamikila kwambili. Lorette anati: “Civomezico cinawononga nyumba yathu na bizinezi yathu. Tinalibe cakudya, koma gulu la Yehova linatithandiza. Linatipatsa zonse zimene tinali kufunikila.” Micheline anati: “Civomezico cinawononga nyumba imene ine na ana anga aŵili tinali kukhalamo. N’nasoŵelatu mtengo wogwila, ndipo n’nali kupemphela kwa Yehova. Iye anayankha pemphelo langa pogwilitsa nchito gulu lake, moti tsopano tili na nyumba yolimba imene timakhalamo. Ndine wotsimikiza mtima kucita zonse zimene ningathe poonetsa ciyamikilo canga kwa Yehova.”

 Akulu-akulu a boma m’delalo anaona thandizo limene tinali kupeleka. Mwacitsanzo, oyang’anila holo yochedwa L’Asile anati: “Nikuyamikilani kwambili pobwela mwamsanga kukapeleka thandizo. Nimakunyadilani cifukwa mumawalemekeza kwambili olamulila a boma, ndipo ndine wokondwa kuona kuti mtima wanu suli pa ndalama koma pa kuthandiza anthu. Mumacita zinthu cifukwa ca cikondi.”

Cimvula ca Mphepo Cochedwa Ana Cinawononga ku Malawi na ku Mozambique

 Pa January 24, 2022, cimphepo ca mkuntho cochedwa Ana cinawononga ku Mozambique kenako cinafalikila mpaka ku Malawi. Cimphepoco cinali kuthamanga makilomita 100 pa ola limodzi ndipo cinabwela na cimvula ca mphamvu. Cimvulaco cinawononga nthambo za malaiti na kukokolola maulalo komanso cinacititsa madzi kusefukila kwambili.

 Cimphepo ca mkunthoco cinakhudza Mboni za Yehova zoposa 30,000 ku Malawi na ku Mozambique. Charles m’bale amene anathandiza pa nchito yopeleka thandizo anati: “N’taona mmene abalewo anali kuvutikila komanso kuculuka kwa zimene anatayikilidwa, cinaniwawa kwambili ndipo n’nasowa cocita.” Zinthu zinafika poipa kwambili cifukwa cakudya cawo cocepa cimene anali naco cinawonongeka, ndipo mbewu zawo zinakokoloka komanso ambili nyumba zawo zinawonongeka. N’zacisoni kuti m’bale mmodzi anataikilidwa mkazi na ana ake aŵili aakazi. Iwo anafa pamene bwato lowapulumutsila linagudubuka.

Nyumba yakugwa ya banja lina ku Mozambique

Nyumba yomanga

 Cimvulaco cinali cocititsa mantha. Usiku ca ku ma 01:00hrs, banja la m’bale Sengeredo amene amakhala ku Nchalo ku Malawi, linamva cimkokomo ca madzi. Mitsinje iŵili inali itasefukila. M’bale Sengeredo anaona kuti ni bwino kuti onse athawe m’nyumbayo. Zimene anacitazo zinali zanzelu cifukwa posakhalitsa madzi osefukila anagwetsa nyumbayo. Katundu wawo anawonongeka ndipo wina anakokoloka. Banjalo linaganiza kuti lipite ku Nyumba ya Ufumu imene ili pa mtunda woyenda mphindi 30 kucokela kunyumba kwawo. Koma panthawiyo, ulendowo unawatengela maola aŵili. Anakafika bwino koma anali atavumbwa kothelatu komanso anali olema.

 Maofesi a nthambi a ku Malawi na ku Mozambique mwamsanga anayamba nchito yopeleka thandizo. Maofesiwo analamula oyang’anila madela komanso akulu kuti afufuze zinthu zimene abale okhudzidwawo anali kufunikila na kuwalimbikitsa. Makomiti angapo othandiza pakagwa tsoka anakhazikitsidwa kuti ayang’anile nchitoyo. Ndipo mwamsanga anayamba kuthandiza abale kuti apeze cakudya na zofunika zina. Ndalama zopitilila madola 33,000, zinagwilitsidwa nchito pothandiza anthu. Ndipo ndalama zopitilila madola 300,000, zinagwilitsidwa nchito pokonza na kumanganso nyumba zowonongeka.

 Makomitiwo anagwilitsa nchito ndalama mwanzelu, ndipo zimenezi zinali zofunika cifukwa zinthu zinali zitakwela mtengo. Mwacitsanzo, miyezi 7 yoyambilila pa nchito yopeleka thandizo, mtengo wa ufa umene ni cakudya cofunika kwambili ku Malawi unakwela na 70 pelesenti. Mtengo wa mafuta a motoka nawonso unakwela. Kuti asawononge ndalama zambili, abalewo anagula zakudya na zomangila ku Malawi komweko komanso anali kugula zambili pa nthawi imodzi. Conco anawacotselako mitengo pa zinthuzo komanso sanawononge ndalama zambili zonyamulila katunduyo.

 Anthu a Yehova anayamilkila kwambili nchito yopeleka thandizo imeneyo. M’bale wina wa ku Mozambique, dzina lake Felisberto, anati: “Sin’naonepo gulu lowolowa manja ngati limeneli, limene lapeleka zipangizo zomangila, mayendedwe, omanga, zakudya komanso malangizo a cikondi. Nchito yopeleka thandizo imeneyi ni citsanzo cocititsa cidwi kwambili ca cikondi ca paubale cimene Yesu anafotokoza pa Yohane 13:34,35.” Ester, mkazi wamasiye wa ku Malawi, amene nyumba yake inagwa anati: “N’nasoŵa mtengo wogwila cifukwa n’nalibe ndalama zoti n’kumangila nyumba ina. Conco pamane abale anabwela na kunimangila nyumba n’namva monga naloŵa kale m’paladaiso.”

 Pamene tikuyandikila dziko latsopano lolonjezedwa, tiyembekeza kuti matsoka acilengedwe adzawonjezeka. (Mateyu 24:7, 8) Ngakhale n’conco, cifukwa ca kuwolowa manja kwanu pocita zopeleka, ndife otsimikiza kuti anthu a Yehova azilandilabe thandizo pakagwa tsoka. Njila zopelekela zopeleka zafotokozedwa pa donate.isa4310.com. Zikomo cifukwa ca kuwolowa manja kwanu.

a Caka cautumiki ca 2022 cinayamba pa September 1, 2021, ndipo cinatha pa August 31, 2022.

b Ndalama zonse zimene zafotokozedwa m’nkhani ino ni madola a ku America.