Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO

Kodi Mboni za Yehova Ndani?

Kodi Mboni za Yehova Ndani?

“Ndinadziŵana ndi Mike kale kwambili. Iye ndi wa Mboni za Yehova. Koma chalichi cimene amapitako cinali kundidabwitsa. Ndinali kudzifunsa kuti: ‘Yehova ndani? N’cifukwa ciani a Mboni sakondwelela maholide? Kodi ndiye kuti Mike wayamba kusokonezeka?’”—Becky, wa ku California, U.S.A.

Pamene aneba anga anayamba kuphunzila Baibulo ndi Mboni za Yehova, Ndinadzifunsa kuti: ‘Kodi dzina lakuti Mboni za Yehova limatanthauza ciani? Dzinali ndi lacilendo kwambili.’”—Zenon wa ku Ontario, Canada.

“Ine ndi mkazi wanga tinali kuganiza kuti Mboni za Yehova zinapezelapo mwai wobwela kunyumba kwathu, cifukwa sitinali kupita ku chalichi. Tinali kuganizanso kuti ngati m’machalichi akuluakulu mulibe zinthu zimene tinali kufunafuna, ndiye kuti kagulu ka m’patuko monga ka Mboni za Yehova sikangakhale nazo.”—Kent wa ku Washington, U.S.A.

“Kukamba zoona, sindinali kudziŵa kuti io ndani ndipo sindinali kudziŵanso zimene amakhulupilila.”—Cecilie wa ku Esbjerg, Denmark.

Mwina inunso mumawaona akulalikila kunyumba ndi nyumba kapena kumalo ena amene kumapezeka anthu ambili, akugaŵila mabuku ofotokoza Baibulo mwina akucititsa phunzilo la Baibulo kwaulele. Kapena munalandilapo magazini ino kucokela kwa mmodzi wa io. Komabe, mwina mumadzifunsa kuti: ‘Kodi Mboni za Yehova ndani makamaka? Mwinanso zimene mumaganiza ndi zofanana ndi zimene ena amene tachula pamwambapa amaganiza.

Ngati muli ndi mafunso ofanana ndi amenewa, kodi mayankho ake mungawapeze kuti? Mungadziŵe bwanji zimene Mboni za Yehova zimakhulupilila? Nanga ndalama zomangila malo ao olambililapo ndi zothandizila nchito yao yolalikila zimacokela kuti? Ndipo n’cifukwa ciani amakulalikilani panyumba panu ndi kumalo ena amene kumapezeka anthu ambili?

Cecilie, amene tamuchula poyamba, anati: “Ndinaŵelenga zinthu zambili pa Intaneti zokhudza Mboni za Yehova komanso ndinamva zinthu zambili zabodza ndi zonyoza anthu amenewa. Cifukwa ca zimenezi, ndinayamba kudana kwambili ndi Mboni za Yehova.” Pambuyo pake, Cecilie, anaganiza zofunsa Mboni za Yehova kuti apeze mayankho okhutilitsa pa mafunso ake.

Kodi mungakonde kudziŵa mayankho azoona pa mafunso anu okhudza Mboni za Yehova? Tikukulimbikitsani kuonana ndi a Mboni za Yehova amene amafalitsa magazini ino, kuti akuuzeni zenizeni. (Miyambo 14:15) Tili ndi cidalilo cakuti nkhani zotsatilazi, zikuthandizani kudziŵa kuti ndife ndani, timakhulupilila zinthu zotani, komanso kudziŵa nchito yathu imene timagwila.