Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mboni za Yehova Ndi Anthu Otani?

Kodi Mboni za Yehova Ndi Anthu Otani?

Ndife gulu lapadziko lonse ndipo sitigwilizana ndi magulu aliwonse a zipembedzo. Ngakhale kuti likulu lathu lili ku United States, Mboni za Yehova zambili zimakhala m’maiko ena. Mboni zoposa 8 miliyoni m’maiko oposa 230 zimaphunzitsa anthu Baibulo. Timacita zimenezi pokwanilitsa mau a Yesu akuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.”Mateyu 24:14.

Mosasamala kanthu za kumene timakhala, timamvela malamulo ndipo sitiloŵelela m’ndale za dziko. Timacita zimenezi cifukwa timamvela mau a Yesu akuti Akristu ‘sayenela kukhala mbali ya dziko.’ Conco sitiloŵelela m’ndale za dziko ndi m’zocitika zina zocilikiza nkhondo. (Yohane 15:19; 17:16) Pa nkhondo yaciŵili ya padziko lonse, Mboni za Yehova zinaikidwa m’ndende, kuzunzidwa ndi kuphedwa cifukwa cokana kuloŵelela m’ndale za dziko. Bishopu wina wa ku Germany analemba kuti: “Iwo ayeneladi kunena kuti cipembedzo cao cokha n’cimene cinakanitsitsa kumenya nao nkhondo mu ulamulilo wa Hitler.”

“[Mboni za Yehova] zili ndi makhalidwe abwino kwambili. Timalakalaka kugwilitsila nchito anthu amenewa pa nkhani za ndale, koma sizingatheke. . . . Zimalemekeza maboma olamulila koma zimakhulupilila kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene ukhoza kuthetsa mavuto onse a mtundu wa anthu.”—Anatelo Nová Svoboda, wofalitsa nkhani ku Czech Republic.

Ngakhale n’conco, sitidzipatula pa anzathu. Yesu anapemphelela ophunzila ake kuti: “Sindikupempha kuti muwacotse m’dziko, koma kuti muwayang’anile kuopela woipayo.” (Yohane 17:15) Mwina mumationa tikugwila nchito, tikupita kusukulu, ndi kugula zinthu m’dela limene timakhala.