Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NJILA YOPEZELA CIMWEMWE

Kukhululuka

Kukhululuka

“PAMENE N’NALI MWANA, N’NALI KUMVA MAU OTUKWANA NA KUNYOZANA M’BANJA MWATHU. Sin’naphunzile kukhululukila ena. Olo pamene n’nakula, nthawi zina n’nali kupitiliza kuganizila zimene wina wanilakwila kwa masiku angapo, kucita kusoŵa tulo,” anakamba conco mayi wina dzina lake Patricia. Kukamba zoona, umoyo wokhala wokhumudwa na kusunga cakukhosi, si umoyo wacimwemwe ndipo umaononga thanzi. Kafukufuku aonetsa kuti anthu amene sakhululuka . . .

  • Amalola mkwiyo na kukhumudwa kuononga maubwenzi awo ndipo zimenezi zimalengetsa munthu kudzipatula na kusungulumwa

  • Amakhumudwa mwamsanga, kukhala na nkhawa, komanso kuvutika maganizo maningi

  • Amakhazikika maningi pa cimene calakwika, cakuti sakhala na umoyo wacimwemwe

  • Amakhala alibe mtendele wa m’maganizo cifukwa codziŵa kuti cinthu coyenela kucita ni kukhululuka

  • Amakhala opanikizika maganizo kwambili ndipo cimakhala cosavuta kudwala matenda amene angaphatikizepo BP, matenda a mtima, na kumva kuŵaŵa m’thupi monga nyamakazi, na kumva mutu kuŵaŵa *

KODI KUKHULULUKA KUMATANTHAUZA CIANI? Kukhululuka kumatanthauza kuiŵalako zimene wina watilakwila na kucotsa mkwiyo, cakukhosi, komanso maganizo ofuna kubwezela. Sikutanthauza kucepetsa colakwaco, kulekelela, kapena kunyalanyaza monga kuti sicinacitike. Koma kukhululuka ni cosankha cimene munthu amapanga pambuyo poganizilapo bwino. Zimenezi zimaonetsa kuti ni wokonda mtendele ndipo afuna ubwenzi wake na munthu amene wamulakwila upitilile.

Kukhululuka kumaonetsanso kuti munthu ni womvetsetsa. Munthu amene amakhululuka amamvetsa mfundo yakuti tonse timalakwa, kapena kucimwa, m’mau na m’zocita. (Aroma 3:23) Pomveketsa bwino mfundo imeneyi Baibo imati: “Pitilizani kulolelana ndi kukhululukilana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi cifukwa codandaulila za mnzake.”—Akolose 3:13.

Conco, m’pomveka kuti kukhululuka ni cizindikilo cakuti munthu ali na cikondi, cimene “cimagwilizanitsa anthu mwamphamvu kwambili kuposa cinthu cina ciliconse.” (Akolose 3:14) Kukamba zoona, malinga n’zimene webusaiti ya Mayo Clinic inakamba, kukhululuka . . .

  • Kumathandiza munthu kukhala pa ubwenzi wabwino na ena, kuphatikizapo kukomela mtima munthu amene wamulakwila, kumumvesetsa, na kum’citila cifundo

  • Kumathandiza munthu kukhala na maganizo abwino komanso kudzimva kuti ali pa ubwenzi wabwino na Mulungu

  • Kumacepetsa nkhawa, nkhanza, na kupanikizika maganizo

  • Amakhala na zizindikilo zocepa za matenda ovutika maganizo

OSADZIIMBA MLANDU. Kusadziimba mlandu kungakhale “kovuta kwambili,” koma “n’kofunika ngako ku thanzi la munthu,” la maganizo ndi la thupi. Izi n’zimene linakamba buku lina lakuti, Disability & Rehabilitation. N’ciani cingakuthandizeni kuti musamadziimbe mlandu?

  • Musamayembekezele kucita zinthu mwangwilo, koma vomelezani kuti monga munthu aliyense, na imwe mudzalakwitsa zinthu zina.—Mlaliki 7:20

  • Muziphunzilapo kanthu pa zimene mwalakwitsa kuti musakabwelezenso zimenezo

  • Makhalidwe ena na zizoloŵezi zina zoipa zimatenga nthawi kuti munthu asinthe. Conco, mudziziledzela mtima.—Aefeso 4:23, 24

  • Muzikhala na mabwenzi olimbikitsa ndi okoma mtima, koma amenenso angakuuzeni mosapita m’mbali mukalakwitsa zinthu.—Miyambo 13:20

  • Mukakhumudwitsa munthu wina, muzivomeleza na kupepesa mwamsanga. Mukayanjananso na munthuyo, mudzakhala na mtendele wa m’maganizo.—Mateyu 5:23, 24

MFUNDO ZA M’BAIBO N’ZOTHANDIZA KWAMBILI!

Ataphunzila Baibo, Patricia amene tam’gwila mau kuciyambi anaphunzila kukhululukila ena. Iye anati: “Nimadzimva kuti ndine womasuka ku mkwiyo umene unali utaononga umoyo wanga. Lomba sinivutikanso maganizo komanso sinivutitsanso ŵena. Mfundo za m’Baibo zimatitsimikizila kuti Mulungu amatikonda ndipo amatifunila zabwino.”

Mwamuna wina dzina lake Ron anati: “Zinali zosatheka kulamulila maganizo na zocita za anthu ena. Koma nikanakwanitsa kulamulila maganizo na zocita zanga. Kuti nikhale na mtendele, n’nadziŵa kuti nifunika kusasunga cakukhosi. N’nayamba kuona mtendele na kusunga cakukhosi monga kum’maŵa na ku m’madzulo. N’zosatheka kukhala ku mbali zonse ziŵili pa nthawi imodzi. Tsopano nili na mtendele m’maganizo.”

^ par. 8 Kumene tatenga mfundo izi: Pa webusaiti yochedwa Mayo Clinic ndi Johns Hopkins Medicine komanso m’buku lakuti, Social Psychiatry and Psychiatric Epidemiology.