Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

GALAMUKA! Na. 1 2018 | Njila Yopezela Cimwemwe

KODI TINGAPEZE KUTI MALANGIZO OTITHANDIZA KUKHALA NA UMOYO WACIMWEMWE?

Baibo imakamba kuti: “Wodala ndi munthu amene . . . amakondwela ndi cilamulo ca Yehova, ndipo amaŵelenga ndi kusinkhasinkha cilamulo cake usana ndi usiku.”—Salimo 1:1, 2.

Nkhani 7 zimenezi, zifotokoza mfundo zimene kwa nthawi yaitali zakhala zothandiza maningi kuti munthu akhale wacimwemwe.

 

Mmene Mungaipezele

Kodi mumaona kuti ndimwe munthu wacimwemwe? N’ciani cimapangitsa munthu kukhala wacimwemwe?

Kukhutila Komanso Kupatsa

Ambili amaganiza kuti munthu amakhala wacimwemwe akapeza cuma cambili. Kodi kukhala na ndalama komanso katundu wambili kumabweletsa cimwemwe cokhalitsa? Kodi zocitika zimaonetsa ciani?

Thanzi Labwino na Kupilila

Kodi matenda angapangitse munthu kusoŵa cimwemwe?

Cikondi

Kuonetsana cikondi n’kofunika kwambili kuti munthu akhale wacimwemwe.

Kukhululuka

Umoyo wokhala wokhumudwa na kusunga cakukhosi, si umoyo wacimwemwe ndipo umaononga thanzi.

Colinga ca Moyo

Kupeza mayankho okhutilitsa pa mafunso ofunika kwambili mu umoyo kungatithandize kukhala acimwemwe.

Ciyembekezo

Anthu ambili amakhala alibe cimwemwe cifukwa alibe ciyembekezo cotsimikizika cokhudza tsogolo lawo ndi la okondedwa awo.

Dziŵani Zambili Zokhudza Njila Yopezela Cimwemwe

Pali zinthu zambili zimene zingapangitse munthu kukhala wacimwemwe kapena iyayi. Dziŵani zambili zokhudza webusaiti yamahala imene ingakuthandizeni pa mavuto osiyana-siyana amene mumakumana nawo mu umoyo wanu.