Pitani ku nkhani yake

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Luso la Mleme Loona Zinthu Ndi Makutu

Luso la Mleme Loona Zinthu Ndi Makutu

 Ngakhale kuti mileme imaona, mitundu ina imatha kuzindikira pomwe pali chinthu chinachake ikakhala mumdima potengera phokoso limene likumveka. Zimene zimachitika n’zakuti phokoso limene mleme umatulutsa, limakawomba pa zinthu zomwe zazungulira n’kubwereranso. Ndiye mlemewo ukamva phokoso lobwereralo, umatha kudziwa pamene chinthucho chili. Mwachitsanzo, mileme ina imatha kusiyanitsa udzudzu ndi tizilombo tina potengera liwiro limene kachilomboko kakugwedezera mapiko ake.

 Taganizirani izi: Mileme yambiri imatulutsa phokoso kudzera pakamwa kapena m’mphuno. Phokosolo likagunda chinthu, limabwerera ndipo milemeyi imagwiritsa ntchito makutu ake omwe amaithandiza kudziwa pomwe chinthucho chili. Phokoso lomwe labwereralo limathandiza milemeyo kuona m’maganizo mwake mmene malo onsewo akuonekera. Ngakhale pamene mileme ina ikuchita phokoso, mleme umatha kuzindikira malo omwe chinthu chili, ngati chinthucho chili pamwamba kapena pansi komanso kutalika kwa mtunda womwe chinthucho chili.

 Kuti mleme uthe kugwira zomwe ukufuna, umafunika kuwerengera mosamala kwambiri kutalika kwa mtundawo kuti usaphonye. Akatswiri ena amanena kuti zimenezi n’zosatheka. Komabe, maumboni ena akusonyeza kuti mileme ili ndi luso lotha kuwerengera bwino mtunda ndipo zimenezi zimathandiza kuti izigwira zomwe ikufuna mosavutikira.

 Akatswiri apanga ndodo imene imagwiritsa ntchito mphamvu yamagetsi, yothandiza anthu omwe ali ndi vuto losaona, kuti azitha kuzindikira kutalika kwa mtunda womwe pali zinthu n’cholinga choti asapunthwe kapena kukodwa m’zinthu zomwe zili pamwamba kapena pansi. Akatswiri awiri, a Brian Hoyle ndi a Dean Waters, amene anapanga ndodo yomwe amaitchula kuti ndodo ya mleme, ananena kuti: “Tinatha kupanga ndodo imeneyi potengera luso la mileme lozindikira kutalika kwa mtunda womwe chinthu chinachake chili potengera phokoso lomwe chinthucho chikutulutsa.”

 Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti mileme ikhale ndi luso limeneli, kapena inachita kulengedwa?