Pitani ku nkhani yake

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Khungu la Kanyama Kooneka Ngati Chipwete

Khungu la Kanyama Kooneka Ngati Chipwete

 Kanyama kameneka(sea cucumber) kamakhala m’nyanja kunsi kwa miyala ndipo thupi lake lili ndi zobayabaya. Kanyamaka ndi kochititsa chidwi kwambiri chifukwa thupi lake limafewa ngati phula ndipo kenako limathanso kusintha n’kulimba ngati thabwa m’kanthawi kochepa kwambiri. Kufewaku kumathandiza kuti kanyamaka kazitha kudutsa mosavuta m’tinjira topanikizika kenako n’kulimbitsa thupi lake kuti adani asakagwire. Kanyamaka kamakwanitsa kuchita zimenezi chifukwa khungu lake linapangidwa mochititsa chidwi kwambiri.

 Taganizirani izi: Khungu la kanyama kooneka ngati chipweteka limatha kusintha n’kukhala lolimba kwambiri, lolimba pang’ono kapenanso kukhala lofewa. Kuti zimenezi zitheke, kanyamaka kamalumikiza kapena kumasula timaulusi tomwe tili mu khungu lake. Kamachita zimenezi pogwiritsa ntchito mapuloteni osiyanasiyana olimbitsira kapena kufewetsera khungu.

 Mapuloteni olimbitsira khungu amapangitsa kuti timaulusi ta mukhungulo tilukanelukane n’kukhala ngati tcheni. Zimenezi zimachititsa kuti khungu la kanyamaka likhale lolimba kwambiri. Pamene mapuloteni ofewetsera khungu amamasula timaulusito, zikatero khungu la kanyamaka limafewa. Khungu la kanyamaka limatha kufewa kwambiri mpaka kufika pomaoneka ngati likusungunuka.

 Asayansi akupanga zipangizo zomwe zingathe kugwira ntchito ngati mmene khungu la kanyamaka limagwirira ntchito. Iwo akufuna kupanga tizitsulo tochitira opaleshoni ya muubongo tomwe tingakhale tolimba bwino, tomwenso tikhoza kumafewa akatiika pamalo omwe akufuna popanga opaleshoniyo. Ngati tizitsuloti tingamasinthe moteromo, zingathandize kuti opaleshoniyo iyende bwino kwambiri.

 Kodi mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti khungu la kanyamaka lizichita zinthu modabwitsa chonchi?