Pitani ku nkhani yake

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Mutu Wogometsa wa Nsomba Yotchedwa Remora

Mutu Wogometsa wa Nsomba Yotchedwa Remora

 Nsomba yotchedwa remora imakwanitsa kudzimatirira pathupi la zamoyo zina zam’nyanja n’kuchokapo popanda kuvulaza zamoyo zinazo. Anthu ochita kafukufuku amagoma ndi mmene chiwalo chapadera chomwe chili pamutu wa nsombayi chimagwirira ntchito.

 Taganizirani izi: Nsombayi imatha kumatirira pathupi la zamoyo zina zam’madzi monga shaki, kamba ndiponso nsomba zikuluzikulu posatengera kuti thupi lake ndi lokhakhala kapena losalala. Nsombayi imadya tizilombo ta pakhungu ndiponso tizidutswa ta chakudya cha chamoyo chomwe yadzimatirirako ndipo imakhala yotetezeka kwa adani ake pa nthawi yonseyi. Akatswiri akufufuza kuti adziwe zambiri zokhudza chiwalo chapaderachi. Iwo akufuna adziwe mmene chimathandizira nsombayi kumatirira bwinobwino pakhungu la zamoyo zina zam’madzi popanda kuzivulaza.

 Nsomba zotchedwa remora zamatirira pakhungu la shaki

 Chiwalochi ndi chozungulira ndipo chili pamwamba pa mutu wa nsombayi. M’mbali mwake muli minofu yokhuthala komanso yofewa yomwe imathandiza kuti ikamatirira pachinthu isachoke. Chilinso ndi mizere yomwe ili ndi timinofu tolimba. Timinofuti tikaima, timagunda khungu la chamoyocho ndipo zimenezi zimachititsa kuti nsombayi imatirire zolimba ndipo siigwa ngakhale pamene chamoyocho chikuthamanga kapena kusintha kolowera.

 Asayansi anapanga chipangizo china chofanana ndi chiwalo cha nsombayi atachita chidwi ndi mmene chimagwirira ntchito. Chipangizochi chomwenso ndi chozungulira chimatha kumatirira kuzinthu zosiyanasiyana, kaya zosalala kapena ayi. Poyeserera, anachimata penapake koma chinawavuta kuchichotsa ngakhale kuti anagwiritsa ntchito zipangizo zina zolemera kwambiri, kuwirikiza maulendo oposa handiredi poyerekeza ndi kulemera kwa chipangizochi.

 Zipangizo zamakono zomwe zikupangidwa potengera chiwalochi, zikhoza kugwiritsidwa ntchito m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, atha kupanga tizizindikiro tomwe angamate pa zamoyo komanso zinthu zina zomwe akufuna kufufuza m’nyanja zikuluzikulu. Akhozanso kuika zipangizozi pa zounikira ndiponso zipangizo zina kuti azizimata pansi pa milatho kapena sitima zam’madzi.

 Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti chiwalo chogometsa cha nsomba yotchedwa remora chizitha kumatirira bwinobwino pakhungu la zamoyo zina? Kapena pali winawake amene anachilenga kuti chizitha kuchita zimenezi?