Pitani ku nkhani yake

Kodi Ndi Tchimo Liti Limene Munthu Sangakhululukidwe?

Kodi Ndi Tchimo Liti Limene Munthu Sangakhululukidwe?

Yankho la m’Baibulo

 Munthu amachita tchimo loti Mulungu sangamukhululukire ngati akuchita zinthu zoipa kwambiri ndipo akusonyeza kuti sangasinthe. Kodi zimenezi zingachitike bwanji?

 Mulungu angakhululukire munthu amene walapa tchimo lake n’kusiya zoipa zimene amachita. Angakhululukire munthuyo ngati amakhulupirira Yesu Khristu. (Machitidwe 3:19, 20) Koma nthawi zina munthu akhoza kumachita tchimo n’kufika poipa kwambiri moti sangasinthe. Baibulo limanena kuti munthu ngati ameneyu amakhala ndi “mtima woipa” ndipo chinyengo champhamvu cha uchimo chimakhala chitaumitsa mtima wake. (Aheberi 3:12, 13) Mtima wa munthu ameneyu umakhala ngati mphika wopindika womwe waotchedwa mu uvuni, moti munthu sangathenso kuuwongola. (Yesaya 45:9) Sipangakhalenso chifukwa chokhululukira munthu ameneyu. Choncho, amakhala kuti wachita tchimo lomwe Mulungu sangamukhululukire.​—Aheberi 10:26, 27.

 Atsogoleri achipembedzo a nthawi ya Yesu, anachita tchimo limeneli. Ankadziwa ndithu kuti mzimu wa Mulungu unkathandiza Yesu kuchita zinthu zosiyanasiyana. Koma ngakhale ankadziwa zimenezi, iwo ankanena kuti Yesu ankathandizidwa ndi Satana Mdyerekezi.​—Maliko 3:22, 28-30.

Kodi ndi machimo ati amene Mulungu angakhululukire munthu?

  •  Kunyoza Mulungu chifukwa chosadziwa. Poyamba, mtumwi Paulo anali munthu wonyoza Mulungu. Koma kenako anasintha ndipo ananena kuti: “Anandichitira chifundo chifukwa ndinali wosadziwa ndi wopanda chikhulupiriro.”​—1 Timoteyo 1:13.

  •  Chigololo. Baibulo limanena za anthu ena omwe poyamba ankachita chigololo. Koma atasiya khalidwe loipali, Mulungu anawakhululukira.​—1 Akorinto 6:9-11.

Kodi ndachita tchimo limene Mulungu sangandikhululukire?

 Ngati mumakhumudwa kwambiri mukaganizira machimo amene munkachita poyamba komanso ngati mumafunitsitsa kusintha, ndiye kuti simunachite tchimo loti Mulungu sangakukhululukireni. Mulungu amakhululukira munthu ngakhale atachita tchimo mobwerezabwereza. Angachite zimenezi ngati akuona kuti mtima wa munthuyo udakali wabwino.​—Miyambo 24:16.

 Anthu ena amaganiza kuti anachita tchimo loti Mulungu sangawakhululukire akaona kuti akumangodziimba mlandu chifukwa cha tchimo limene anachitalo. Komabe, Baibulo limasonyeza kuti nthawi zina mtima wathu ukhoza kutipangitsa kumamva ngati tachita tchimo loti Mulungu sangatikhululukire. (Yeremiya 17:9) Choncho ndi bwino kumakumbukira kuti Mulungu sanatipatse udindo woti tiziweruza ena kapena kumadziweruza tokha. (Aroma 14:4, 12) Mulungu akhoza kutikhululukira ngakhale zitakhala kuti mtima wathu ukutiimba mlandu.​—1 Yohane 3:19, 20.

Kodi Yudasi Isikariyoti anachita tchimo loti Mulungu sangamukhululukire?

 Inde. Yudasi anali ndi mtima woipa kwambiri moti ankaba ndalama zomwe anthu ankapereka. Nthawi ina anauza Yesu kuti angachite bwino atagulitsa mafuta onunkhira n’cholinga choti ndalama zake athandizire osauka. Koma sikuti Yudasi ankaganiziradi osaukawo. Iye ankadziwa kuti akagulitsa mafutawo, ndalama zomwe ankasunga zichuluka kwambiri, moti akaba sizidziwika. (Yohane 12:4-8) Kenako Yudasi anafika poipa kwambiri moti pogulitsa Yesu ndi ndalama 30 zasiliva. Yesu ankadziwa kuti Yudasi sangasinthe moti anamutchula kuti “mwana wa chiwonongeko.” (Yohane 17:12) Zimenezi zikusonyeza kuti Yudasi anachita tchimo loopsa limeneli, ndipo Mulungu sadzamuukitsa.​—Maliko 14:21.

 N’zoona kuti Yudasi analapa, koma sikuti analapa kuchokera pansi pamtima. Tikutero chifukwa analapa osati kwa Mulungu, koma kwa atsogoleri achipembedzo amene anagwirizana nawo zogulitsa Yesu.​—Mateyu 27:3-5; 2 Akorinto 7:10.