Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Kuti Munthu Amene Analandira Khristu Ndiye Kuti Basi Sangawonongedwe?

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Kuti Munthu Amene Analandira Khristu Ndiye Kuti Basi Sangawonongedwe?

Yankho la m’Baibulo

 Ayi, Baibulo siliphunzitsa zimenezi. Munthu amene wapulumutsidwa chifukwa chakuti amakhulupirira Yesu Khristu akhoza kutaya chikhulupiriro chake komanso mwayi wake wodzapulumuka. Baibulo limanena kuti munthu ayenera “kumenya mwamphamvu nkhondo” kuti apitirize kukhala ndi chikhulupiriro. (Yuda 3, 5) Akhristu oyambirira amene anali atalandira kale Khristu anauzidwa kuti: “Pitirizani kukonza chipulumutso chanu, mwamantha ndi kunjenjemera.”—Afilipi 2:12.

Malemba sasonyeza kuti munthu akalandira Khristu ndiye kuti sangawonongedwenso

  •   Baibulo limachenjeza za machimo akuluakulu amene angachititse kuti munthu asadzalowe mu Ufumu wa Mulungu. (1 Akorinto 6:9-11; Agalatiya 5:19-21) Chenjezo limeneli likanakhala losamveka zikanakhala kuti munthu akalandira Khristu ndiye kuti sangatayenso chipulumutso chake. Koma Baibulo limanena kuti munthu amene analandira Khristu akhoza kutaya chipulumutso chake ngati atayamba kuchita machimo akuluakulu. Mwachitsanzo, Aheberi 10:26 limati: “Ngati tikuchita machimo mwadala pambuyo podziwa choonadi molondola, palibe nsembe ina yotsala imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo.”—Aheberi 6:4-6; 2 Petulo 2:20-22.

  •   Yesu anagwiritsa ntchito fanizo la mtengo wa mpesa pofuna kufotokoza kufunika kopitiriza kukhala ndi chikhulupiriro. Iye anadziyerekezera ndi mtengo wa mpesawo ndipo ophunzira ake anawayerekezera ndi nthambi za mtengowo. Ophunzira ake ena anasonyeza ndi zipatso zawo, kapena kuti zochita zawo, kuti ali ndi chikhulupiriro koma kenako anasintha ndipo ‘anaponyedwa kunja monga nthambi’ yosabala zipatso n’kutaya chipulumutso chawo. (Yohane 15:1-6) Paulo anagwiritsanso ntchito fanizo lofanana ndi limeneli ndipo ananena kuti Akhristu amene sakupitiriza kukhala ndi chikhulupiriro ‘adzadulidwa.’—Aroma 11:17-22.

  •   Baibulo limanena kuti Akhristu ayenera ‘kukhalabe maso.’ (Mateyu 24:42; 25:13) Anthu amene amagona mwauzimu ndipo amachita “ntchito za mdima” kapena kulephera kuchita zinthu zina zimene Yesu analamula, amataya mwayi wawo wodzapulumuka.—Aroma 13:11-13; Chivumbulutso 3:1-3.

  •   Malemba ambiri amasonyeza kuti anthu amene apulumutsidwa amafunika kupirirabe mpaka mapeto. (Mateyu 24:13; Aheberi 10:36; 12:2, 3; Chivumbulutso 2:10) Akhristu oyambirira anasangalala kwambiri atamva kuti Akhristu anzawo akupirirabe mwachikhulupiriro. (1 Atesalonika 1:2, 3; 3 Yohane 3, 4) Ndiye kodi n’zomveka kuti Baibulo lingamalimbikitse anthu kuti akhalebe okhulupirika mpaka mapeto ngati n’zoona kuti anthu amene sangapirire adzapulumukabe?

  •   Mtumwi Paulo atatsala pang’ono kumwalira m’pamene anayamba kutsimikizira kuti adzapulumuka. (2 Timoteyo 4:6-8) Koma asanafike pa nthawiyi, ankadziwa kuti sangapulumuke ngati atayamba kutsatira zilakolako za thupi lake. N’chifukwa chake analemba kuti: “Ndikumenya thupi langa ndi kulitsogolera ngati kapolo, kuopera kuti, pambuyo poti ndalalikira kwa ena, ineyo ndingakhale wosayenera m’njira inayake.”—1 Akorinto 9:27; Afilipi 3:12-14.