Pitani ku nkhani yake

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Nkhani Yovomereza Ana Kugwiritsa Ntchito Intaneti—Gawo 2: Kuphunzitsa Mwana Wanu Wachinyamata Kukhala Wosamala Pogwiritsa Ntchito Intaneti

Nkhani Yovomereza Ana Kugwiritsa Ntchito Intaneti—Gawo 2: Kuphunzitsa Mwana Wanu Wachinyamata Kukhala Wosamala Pogwiritsa Ntchito Intaneti

 Chifukwa choganizira mavuto amene amakhalapo anthu akamagwiritsa ntchito intaneti, makolo ambiri salola kuti ana awo aziigwiritsa ntchito. Komabe, ngati mwalola kuti mwana wanu wachinyamata azigwiritsa ntchito intaneti, kodi mungamuthandize bwanji kupewa zinthu zoipa zimene zingakhalepo chifukwa chogwiritsa ntchito intaneti komanso zomwe angachite kuti aziigwiritsa ntchito bwino?

Zimene zili munkhaniyi

 Zimene Mwana wanu amaona kukhala zofunika kwambiri

 Zimene muyenera kudziwa: Poti anthu ambiri sachedwa kutengeka komanso kuyamba kukonda kwambiri intaneti, m’pofunika kuthandiza mwana wanu kuchepetsa nthawi imene amakhala pa intaneti.

 Lemba Lothandiza: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”—Afilipi 1:10.

 Zoti muganizire: Kodi mwana wanu amalephera kugona, kulemba za kusukulu kapena kucheza ndi anthu pakhomo chifukwa choti amangokhalira pa intaneti? Ochita kafukufuku ena ananena kuti achinyamata amafunika kuti azigona pafupifupi maola 9, koma n’kutheka kuti amene amakhala nthawi yaitali pa intaneti sakwanitsa n’komwe maola 7.

 Zimene mungachite: Kambiranani ndi mwana wanu wachinyamata zimene zili zofunika kwambiri komanso za kufunika kochepetsa nthawi imene amakhala pa intaneti. Ikani malamulo othandiza monga akuti pokagona asamalowe kuchipinda ndi chipangizo china chilichonse. Cholinga chanu ndi kumuthandiza kukhala wodziletsa. Khalidweli lidzamuthandiza kwambiri akakula.—1 Akorinto 9:25.

 Mmene zingakhudzire maganizo a mwana wanu

 Zimene muyenera kudziwa: Wachinyamata amene amangokhalira kuona zithunzi zadijito zokonzedwa bwino zomwe anzake adzijambula komanso zosonyeza kuti akusangalala, sakhala wosangalala, amakhala wokhumudwa ndiponso amavutika maganizo.

 Lemba lothandiza: “Lekani . . . kaduka.”—1 Petulo 2:1.

 Zoti muganizire: Kodi intaneti imapangitsa kuti mwana wanu wachinyamata azidziyerekezera ndi anthu ena pa nkhani ya mmene amaonekera ndiponso mmene thupi lake lili? Kodi mwana wanuyo amaona kuti anthu onse amakhala osangalala kusiyana ndi iyeyo?

 Zimene Mungachite: Kambiranani ndi mwana wanu za kuipa kodziyerekezera ndi anthu ena. Dziwani kuti atsikana ndi amene amakhudzidwa kwambiri ndi vutoli kusiyana ndi anyamata. Izi zili chonchi chifukwa atsikana amaganizira kwambiri zonena za anzawo komanso za mmene matupi awo akuonekera. Mukhoza kuuza mwana wanu kuti azipumira kaye kwa kanthawi asanayambirenso kugwiritsa ntchito intaneti. Mnyamata wina dzina lake Jacob anati: “Kwa nthawi ndithu ndinadilita apu yanga ndipo ndinasiya kugwiritsa ntchito intaneti. Izi zinandithandiza kusintha mmene ndinkaonera zinthu zofunika kwambiri, mmene ndinkadzionera komanso mmene ndinkaonera anthu ena.”

 Zochita za mwana wanu pa intaneti

 Zimene muyenera kudziwa: Kukhala pa intaneti kuli ngati kukhala pachigulu cha anthu. Kusamvetsetsana komanso kuyambana kumatha kuyambika nthawi iliyonse pagulu la anthu.

 Lemba Lothandiza: “Kuwawidwa mtima konse kwa njiru, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe zichotsedwe mwa inu . . . Khalani okomerana mtima.”—Aefeso 4:31, 32.

 Zoti muganizire: Kodi intaneti yapangitsa mwana wanu wachinyamata kukonda miseche, mikangano kapenanso kusalankhula bwino?

 Zimene mungachite: Muthandizeni mwana wanu kudziwa kugwiritsa ntchito bwino intaneti. Buku lina linanena kuti: “Ndi udindo wathu monga makolo kuphunzitsa momveka bwino mwana kudziwa kuti kuchitira nkhanza anthu ena ndi kosavomerezeka. Kaya zimenezi zichitikire pa intaneti kapena pamasom’pamaso.”—Digital Kids.

 Muzikumbukira kuti ndi zotheka kukhala bwinobwino popanda kugwiritsa ntchito intaneti ndipo si makolo onse amene amalola ana awo achinyamata kuti aziigwiritsa ntchito. Ngati mwalola kuti mwana wanu azigwiritsa ntchito intaneti, onetsetsani kuti ndi wokhwima maganizo moti akhoza kudziikira malire a nthawi imene azikhala pa intaneti, akhoza kukhala ndi anzake abwino ndiponso kupewa zinthu zoipa.