Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Vladimir Balabkin (pakati) ndi mkazi wake Tatyana, limodzi ndi achibale komanso anzawo, panja pa khoti m’baleyu atatulutsidwa m’ndende

25 DECEMBER 2023
RUSSIA

M’bale Vladimir Balabkin Wazaka 71 Watulutsidwa M’ndende

M’bale Vladimir Balabkin Wazaka 71 Watulutsidwa M’ndende

Pa 19 December 2023, M’bale Vladimir Balabkin anatulutsidwa m’ndende pambuyo pogwira ukaidi kwa miyezi yopitirira itatu yokha ngakhale kuti anagamulidwa kuti akhale m’ndende zaka 4. M’baleyu anaikidwa m’ndende pa 13 September 2023. Khoti litapereka chigamulo chake, M’bale Balabkin anachita apilo za chigamulochi. Oweruza atatu amene anamvetsera apilo yake anasintha chigamulo choyamba chija. Choncho, chilango chake chinachepetsedwa kuchokera pa zaka 4 zokakhala m’ndende n’kungouzidwa kuti kwa chaka chimodzi azitsatira malamulo ena a khoti ali kunyumba kwawo.

Pa nthawi imene khoti linkazenga mlandu wake, M’bale Balabkin ananena molimba mtima kuti: “Zimene ndimakhulupirira zimachokera m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Ndipo Baibulo landithandiza kukhala ndi makhalidwe amene Mlengi amayembekezera kuti anthu onse akhale nawo monga kudekha, kukoma mtima, kuleza mtima komanso kudziletsa. Baibulo lathandiza kwambiri ineyo ndi banja langa. Ndikufuna kuti aliyense awadziwe bwino Mawu a Mulungu chifukwa angathandize aliyense kusintha moyo wake n’kumachita zinthu zabwino kwambiri.”

Tikusangalala ndi M’bale Balabkin limodzi ndi banja lake ndipo tikupitiriza kupempherera onse amene adakali m’ndende podziwa kuti Yehova adzawadalitsa chifukwa cha kupirira kwawo.​—Aheberi 10:34.