Pitani ku nkhani yake

JUNE 29, 2021
MOZAMBIQUE

Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu Latulutsidwa mu Chinyungwe

Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu Latulutsidwa mu Chinyungwe

Pa 27June 2021, M’bale Adão Costa, wa m’Komiti ya Nthambi ya ku Mozambique, anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la mu Chinyungwe. Baibuloli ndi la pazipangizo zamakono ndipo linatulutsidwa pa pulogalamu yochita kujambuliratu. Ofalitsa oposa 2,600 anaonera pulogalamuyi kudzera pa intaneti ndipo inaulutsidwanso pa TV komanso pawailesi.

Mfundo Zina Zokhudza Ntchito Yomasulira Baibuloli

  • Chinyungwe chimalankhulidwa kumpoto chakumadzulo kwa Mozambique, m’dera la Tete

  • Anthu pafupifupi 400,000 amalankhula Chinyungwe

  • Omasulira 6 anagwira ntchito yomasulira Baibuloyi kwa zaka ziwiri

M’bale Costa anati: “Kwa zaka zambiri tinalibe Baibulo la m’chilankhulo cha Chinyungwe. Choncho abale ndi alongo achilankhulochi ankagwiritsa ntchito Baibulo la Chichewa. Zimenezi zinali zovuta kwambiri chifukwa sankamvetsa bwino mawu ambiri a Chichewa.”

Baibuloli lisanatulutsidwe, mmodzi mwa omasulira ananena kuti: “Ofalitsa akadzalandira Baibuloli adzajowajowa chifukwa cha chisangalalo. Kwa iwo, zidzakhala ngati maloto, zozizwitsa zochokera kwa Yehova. Ndipo adzathokoza kwambiri Yehova.”

Ndi pemphero lathu kuti Baibuloli lithandize anthu ambiri amtima wabwino kuti apindule ndi uthenga wake.​—Chivumbulutso 22:17.