Pitani ku nkhani yake

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Mphotho Yaikulu Kwambiri pa Moyo Wanga

Mphotho Yaikulu Kwambiri pa Moyo Wanga
  • CHAKA CHOBADWA 1967

  • DZIKO FINLAND

  • POYAMBA ANALI KATSWIRI WA MASEWERA A TENESI

KALE LANGA

 Ndinakulira kudera la kumudzi ku Tampere, m’dziko la Finland. Kuderali ndi kwa phee ndiponso kumaoneka kobiriwira chifukwa cha zomera. Banja lathu silinkakonda zopembedza komabe tinkaona kuti maphunziro komanso makhalidwe abwino ndi ofunika kwambiri. Mayi anga ndi a ku Germany koma nthawi zambiri ndinkakonda kukhala kwa agogo anga ku West Germany.

 Ndinayamba kukonda masewera ndili mwana. Poyamba ndinkangosewera masewera alionse koma nditakwanitsa zaka 14 ndinasankha kuti ndidziwe zambiri za masewera a tenesi. Ndili ndi zaka 16 ndinayamba kuphunzira masewerawa kawiri kapena katatu patsiku. Akatswiri ankandiphunzitsa maulendo awiri patsiku kenako madzulo ake ndinkakayeserera pandekha. Ndinkachita chidwi ndi zinthu zingapo zomwe zimachitika posewera tenesi. Masewera a tenesi ankandithandiza kukhala wathanzi komanso woganiza bwino. Ndinkasangalala kucheza ndi anzanga komanso kumwako mowa mwa apa ndi apo. Nthawi zina ndinkagwiritsanso ntchito mankhwala osokoneza bongo koma osati kwambiri moti sanandibweretsere mavuto alionse. Maganizo anga onse anali pa tenesi.

 Nditafika zaka 17 ndinayamba kuchita nawo mipikisano yomwe Bungwe Loona za Akatswiri Osewera Tenesi linakhazikitsa. a Ndinakhala katswiri wotchuka kwambiri chifukwa chowina mipikisano ingapo. Pamene ndinkakwanitsa za 22 ndinali mmodzi wa akatswiri 50 odziwa kusewera tenesi padziko lonse.

 Kwa zaka zambiri ndakhala ndikupita m’mayiko osiyanasiyana kukasewera tenesi monga katswiri. M’mayiko omwe ndinkayendawo ndinkaona zinthu zina zosangalatsa. Komabe ndinkakhudzidwa ndi mavuto omwe anthu akukumana nawo chifukwa chochitiridwa nkhanza, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso kuwonongeka kwa chilengedwe. Mwachitsanzo, nthawi ina titapita ku United States tinauzidwa kuti tisayerekeze kufika madera enaake chifukwa choti kunkachitika zauchigawenga. Zinthu ngati zimenezi zinkandikhumudwitsa kwambiri. Ngakhale kuti ndinkachita masewera omwe ndinkawakonda, tsiku likamatha, ndinkangomva kuti ndikuperewera zinazake.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA

 Pa nthawiyo, Sanna yemwe anali chibwenzi changa anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Ndinadabwa kumuona kuti wayamba kukonda zimene akuphunzira, koma sindinamuletse. Mu 1990, tinakwatirana ndipo chaka chotsatira Sanna anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova. Ineyo ndinkakhulupirira ndithu kuti Mulungu alipo, koma nkhani zachipembedzo sizinkandikhudza. Ndinkakumbukiranso kuti agogo anga ankakonda kuwerenga Baibulo, moti nthawi ina anandiphunzitsa kupemphera.

 Tsiku lina, ine ndi mkazi wanga Sanna tinakacheza ndi banja lina la Mboni. Ndiyeno mwamuna wa banjalo dzina lake Kari, anandifotokozera za ulosi wa m’Baibulo wonena za “masiku otsiriza.” (2 Timoteyo 3:1-5) Zimene anandiuzazo zinandichititsa chidwi kwambiri ndipo zinandithandiza kuzindikira chifukwa chake padzikoli pakuchitika zinthu zambiri zoipa. Tsiku limenelo sitinakambirane kwambiri zokhudza chipembedzo. Kuchokera nthawi imeneyo, ndinayamba kumufunsa Kari zinthu zambiri zokhudza Baibulo ndipo zonse zomwe ankandiphunzitsa zinkandifika pamtima. Koma chifukwa choti ndinkakhala otanganidwa komanso ndinkakonda kuyendayenda, zinachititsa kuti tisamakune pafupipafupi. Koma Kari sanatope nane. Nthawi zina ankandilembera kalata poyankha mafunso omwe ndinamufunsa pa nthawi yomwe ankandiphunzitsa. Anayankhanso mafunso anga onse ovuta okhudza moyo pogwiritsa ntchito Baibulo. N’kupita kwa nthawi ndinadziwa kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzathetse mavuto onse. Ndinasangalala kudziwa kuti dzina la Mulungu ndi Yehova komanso kuti pali zinthu zabwino zomwe amatichitira. (Salimo 83:18) Ndinasangalalanso kwambiri kudziwa kuti Mulungu anapereka dipo. Sikuti analipereka pongofuna kukonza zinthu, koma pofuna kusonyeza kuti amatikonda kwambiri. (Yohane 3:16) Ndinaphunziranso kuti n’zotheka kukhala bwenzi la Mulungu komanso kudzalandira moyo wosatha m’paradaiso n’kumadzakhala mwamtendere. (Yakobo 4:8) Kenako ndinayamba kudzifunsa kuti, “Kodi ndingasonyeze bwanji kuti ndimayamikira zimenezi?”

 Ndinayamba kuganizira kwambiri za mmene ndimachitira zinthu pa moyo wanga. Baibulo linandithandiza kudziwa kuti munthu amasangalala chifukwa chokhala opatsa. Ndiyeno ndinaona kuti ndi bwino kuti ndiziuzako ena zomwe ndimakhulupirira. (Machitidwe 20:35) Popeza kuti ndinali katswiri wa tenesi, ndinkangokhalira kupita ku mipikisano yosiyanasiyana moti pafupifupi masiku 200 pachaka, sindinkapezeka panyumba. Banja lathu lonse linkatanganidwa kuti lindithandize pokonzekera masewerawa komanso ndikakhala ndi ulendo wopita kumipikisano. Ndinazindikira kuti ndikufunika kusintha moyo wanga.

 Ndinkadziwa kuti anthu ena sadzamvetsa ndikasiya kusewera tenesi chifukwa choti ndayamba kuchita zinthu zokhudzana ndi chipembedzo. Koma ndinkaona kuti kudziwa bwino Yehova komanso lonjezo loti tidzakhala ndi moyo wosatha n’kofunika kwambiri kuposa mphoto iliyonse imene ndingapeze chifukwa chopambana pa masewera a tenesi. Poganizira zimenezi sizinandivute kusiya tenesi. Ndinaona kuti nditseke makutu kuti ndisamve zonena za anthu zokhudza zimene ndasankha. Lemba la Salimo 118:6 ndi limene linandithandiza kupirira zonena za anthu. Limanena kuti: “Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa. Munthu wochokera kufumbi angandichite chiyani?”

 Pa nthawiyi, mabungwe ena omwe ankandithandiza anandipatsa mwayi womwe ukanachititsa kuti ndizipeza ndalama zambiri. Popeza kuti ndinali katswiri, zimenezi zikanachititsa kuti ndizikhala mosangalala kwa zaka zambiri. Komabe ndinali nditasankha kale zochita moti ndinakana mwayi umenewo. Pasanapite nthawi ndinasiyanso kuchita nawo mipikisano ya m’Bungwe Loona za Akatswiri Osewera Tenesi. Ndinapitiriza kuphunzira Baibulo ndipo pa 2 July 1994, ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA

 Sindinachite kulimbalimba kuti ndiyambe kuphunzira za Mulungu. Komanso sikuti ndinkachita kulakalaka kuti ndiphunzire choonadi. Ndinkaona kuti zonse zili bwino pa moyo wanga. Koma mosayembekezereka zinthu zinasintha ndipo ndinayamba kuona kuti moyo ndi wofunika kwambiri. Zinangokhala ngati choonadi cha m’Baibulo chinkandidikirira kuti ndichipeze. Panopa ndikusangalala kwambiri ndiponso banja lathu ndi logwirizana kuposa kale. Chosangalatsa chinanso n’chakuti nawonso ana anga atatu akuyesetsa kukonda Mulungu koma osati masewera a tenesi.

 Sikuti ndinasiyiratu kusewera tenesi. Kwa zaka zambiri ndakhala ndikupeza kangachepe kuchokera m’zochitika zosiyanasiyana zokhudza tenesi. Mwachitsanzo, nthawi zina ndimakhala kochi kapenanso woyang’anira masewerawa. Sikuti moyo wanga wonse umangokhala pa zamasewera. Ndisanaphunzire choonadi, wiki iliyonse ndinkangokhalira kuphunzira masewera a tenesi kwa maola ambiri n’cholinga choti ndikhale katswiri. Panopa ndikuchita utumiki wa nthawi zonse ndipo ndimasangalala kugwiritsa ntchito nthawi yanga pothandiza anthu kuphunzira komanso kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo, zomwenso zinandithandiza kusintha moyo wanga. Chinthu chofunika kwambiri pa moyo wanga ndi kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova Mulungu komanso kuuza ena za tsogolo labwino limene tikuliyembekezera.​—1 Timoteyo 6:19.

a Bungwe Loona za Akatswiri Osewera Tenesi ndi lomwe limayang’anira akatswiri a amuna osewera tenesi m’madera osiyanasiyana. Bungweli limakhala ndi m’ndandanda wa akatswiri komanso mipikisano yosiyanasiyana ndipo amapereka mphoto kwa owina potengera mapointi omwe apeza. Akawerengetsera mapointi omwe osewera apeza pa mipikisano yomwe inakhazikitsidwa, amasankha omwe akuyenera kuikidwa pam’ndandanda wa akatswiri a tenesi padziko lonse.