Pitani ku nkhani yake

Kodi Nyumba ya Ufumu Ingathandize Bwanji Anthu M’dera Lanu?

Kodi Nyumba ya Ufumu Ingathandize Bwanji Anthu M’dera Lanu?

A Mboni za Yehova akhala akulemba mapulani komanso kumanga okha nyumba zolambiriramo kwa zaka zoposa 100. Kodi m’dera lanu mukumangidwa malo olambiriramo amenewa omwe amatchedwa kuti Nyumba ya Ufumu? Kodi Nyumba ya Ufumu ingakuthandizeni bwanji m’dera lanu?

Ofesi ya Nthambi ya Flowery, ku Georgia, U.S.A.

“Mphatso Yooneka Bwino M’deralo”

Nyumba za Ufumu zimamangidwa mwa njira yoti ziziwonjezera kukongola kwa dera limene nyumbazo zamangidwa. A Jason omwe amayang’anira ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ku United States anati: “Cholinga chathu n’choti Nyumba ya Ufumu iliyonse izioneka bwino m’dera limene yamangidwa.” Wa mboni wina yemwe amagwira ntchito ndi gulu lojambula mapulani ananenanso kuti: “Timafuna kuti nyumba yomwe tamanga izikhala mphatso yooneka bwino m’deralo komanso isamakhale yochititsa manyazi poyerekezera ndi nyumba zina kuderalo.”

Nyumba za Ufumu zimamangidwa ndi a Mboni za Yehova ongodzipereka omwe amagwiritsa ntchito nthawi ndi maluso awo komanso amafunitsitsa kumanga nyumba zabwino kwambiri. Anthu ena amaona luso lawo pa nyumba yomwe amanga. Mwachitsanzo, posachedwapa Nyumba ya Ufumu ina itamangidwa mumzinda wa Richmond ku Texas, U.S.A., bambo wina yemwe amagwira ntchito yofufuza mmene anthu amangira nyumba m’deralo, ananena kuti denga la Nyumba ya Ufumuyo ndi limodzi mwa madenga okhomedwa bwino kwambiri omwe anawaonapo. Ku Jamaica, munthu wina yemwe amagwira ntchito yofufuza mmene anthu amangira nyumba anatengana ndi gulu la anthu amene angoyamba kumene ntchitoyo kuti akayendere ntchito yomanga Nyumba ya Ufumu ina. Atafika anauza anthu amene anali nawowo kuti: “Anthu amenewa musadandaule nawo. A Mboni za Yehova amamanga motsatira mapulani ndipo amathanso kumanga bwino kwambiri kuposa zimene malamulo a zomangamanga a m’dera lawo amafuna.” Bambo wina yemwe amagwira ntchito yofufuza mmene anthu amangira nyumba munzinda wina ku Florida, U.S.A., anati: “Ndakhala ndikuyendera ntchito yomanga zipatala komanso ntchito zikuluzikulu za boma koma sindinaone anthu akugwira ntchito mwadongosolo ngati mmene mukuchitiramu. Anthu inu mumagwira bwino ntchito.”

Ku Concession, Zimbabwe

Nyumba ya Ufumu Imathandiza Kwambiri Anthu

Misonkhano yomwe imachitika mu Nyumba ya Ufumu imathandiza kwambiri anthu omwe amapezeka pamisonkhanoyo. Misonkhanoyi yathandiza anthu omwe ali ndi ana kukhala makolo abwino komanso yathandiza ana kukhala omvera makolo. A Rod omwe amagwira ntchito ndi gulu lojambula mapulani a Nyumba za Ufumu ananena kuti: “Nyumba ya Ufumu iliyonse ndi malo ophunzitsirako anthu makhalidwe abwino ndipo anthu a madera ozungulira amapindula ndi zimenezi.” Iwo ananenanso kuti: “Anthu amaphunzirako zimene zingawathandize akamakumana ndi mavuto pamoyo wawo. Ukalowa m’Nyumba ya Ufumu umapeza anthu ansangala komanso a chikondi ndipo zimenezi zimathandiza anthu onse omwe akufuna kutonthozedwa ndi kudziwa za Mulungu kuti akhale omasuka.”

Anthu amene amasonkhana m’Nyumba za Ufumu amadera nkhawa anthu ena ndipo pakachitika ngozi zadzidzidzi, amawathandiza mwachangu. Mwachitsanzo, mu 2016 ku Bahamas kutachitika chimphepo chamkuntho (Hurricane Matthew), a Mboni za Yehova anakonza nyumba za anthu zokwana 254 zomwe zinaonongeka. M’dera lina, mayi ena a zaka 80 dzina lawo a Violet, m’nyumba yawo munalowa madzi ndipo anapita kwa a Mboni omwe ankathandiza anthu okhudzidwa ndi mphepoyo. Iwo anauza a Mboniwo kuti awalipira ngati angawathandize. A Mboniwo anakonza denga la nyumba ya mayiwo kuti lisamadonthe koma sanalole kuti awapatse ndalama iliyonse. Kenako anaika khoma lamatabwa latsopano kuti athe kukonza siling’i ya chipinda chochezera. Ntchitoyo itatha, a Violet anakumbatira wa Mboni aliyense amene anagwira nawo ntchitoyo, ndipo anawathokoza maulendo ambirimbiri kwinaku akunena kuti, “Inu ndinudi anthu a Mulungu!”

Ku Bad Oeynhausen, North Rhine-Westphalia, Germany

‘Ndife Osangalala Kuti Nyumba ya Ufumuyi Ili M’dera Lathu’

Pofuna kuthandiza kuti Nyumba za Ufumu zizioneka bwino nthawi zonse, a Mboni za Yehova amaphunzitsa mpingo womwe umagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu iliyonse mmene angamasamalire ndi kukonzera nyumbayo. Kuchita zimenezi kwathandiza kwambiri. Mwachitsanzo, m’dera lina laling’ono ku Arizona, U.S.A., mayi wina anavomera a Mboni atamuitana kuti akasonkhane nawo ku Nyumba ya Ufumu. Iye anayamikira kuti nyumbayo inkasamaliridwa bwino, komanso anasangalala atamva kuti pali ndondomeko yosamalirira nyumbayo ndiponso kuti a Mboniwo akugwira ntchito yokonza nyumbayo ngakhale kuti inali ikuoneka kale bwino. Mayiyu anali mtolankhani wa nyuzipepala inayake ndipo anadzalemba m’nyuzipepalayo lipoti loyamikira mmene a Mboni amasamalirira ndi kukonzera Nyumba ya Ufumu. Mayiyo anamaliza lipotilo ndi mawu akuti, “Ndife osangalala kuti . . . Nyumba ya Ufumuyi ili m’dera lathu.”

Nyumba za Ufumu zimapezeka m’madera osiyanasiyana padziko lonse lapansi. Tikukulimbikitsani kuti mupite ku Nyumba ya Ufumu iliyonse yomwe mungakwanitse kufikako. Ndipo mukalandiridwa ndi manja awiri.