Mboni za Yehova Padziko Lonse

Italy

  • Mzinda wa Venice, m’dziko la Italy​—Akulalikira pogwiritsa ntchito Baibulo

Mfundo Zachidule—Italy

  • 58,851,000—Chiwerengero cha anthu
  • 250,193—Chiwerengero cha Mboni za Yehova
  • 2,804—Mipingo
  • Pa anthu 236 alionse pali wa Mboni za Yehova m’modzi

NKHANI

Ku Italy Kunachitika Mwambo Wokumbukira a Mboni za Yehova Omwe Anazunzidwa ndi Chipani cha Nazi

Mwambo wokumbukira a Mboni za Yehova masauzande omwe anazunzidwa ndi chipani cha Nazi kumayiko a ku Europe unachitikira pa Risiera di San Sabba mumzinda wa Trieste ku Italy.

NKHANI

Khoti Lalikulu Kwambiri ku Italy Lagamula Kuti a Mboni za Yehova Ali ndi Ufulu Wopanga Zosankha pa Nkhani ya Chithandizo Chamankhwala

Chigamulo chaposachedwapa chinapereka ufulu kwa abale athu wopanga zosankha pa nkhani yokhudza chithandizo chamankhwala chomwe akufuna.

NKHANI

Madokotala ku Italy Anasonyeza Chidwi pa Nkhani Yothandiza Odwala Popanda Kuwaika Magazi

Misonkhano iwiri imeneyi inathandiza kuti akatswiri ambiri azachipatala adziwe njira zatsopano zokhudza kuthandiza odwala popanda kugwiritsa ntchito magazi. Komanso, madokotala opanga maopaleshoni anafotokozera abale ndi alongo zinthu zabwino zomwe akhala akukumana nazo akamagwira ntchito ndi a Mboni za Yehova.

GALAMUKANI!

Dziko la Italy

Dziko la Italy limadziwika ndi zinthu zakale, madera osiyanasiyana komanso kuli anthu okonda kucheza. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zambiri za dzikoli komanso zokhudza Mboni za Yehova za kumeneko.