Pitani ku nkhani yake

Kodi Paukwati wa Mboni za Yehova Pamachitika Zotani?

Kodi Paukwati wa Mboni za Yehova Pamachitika Zotani?

Nthawi zambiri paukwati wa Mboni za Yehova pamakambidwa nkhani yachidule yochokera m’Baibulo ndipo umenewu umakhala mwambo wosavuta komanso wolemekezeka. Mwambowu ukatha, pamakhala phwando. a Yesu anapezeka paphwando laukwati mumzinda wa Kana pa nthawi yomwe ankayamba kumene utumiki wake.—Yohane 2:1-11.

 Kodi pamwambo waukwati pamachitika zotani?

Pamwambowu pamakambidwa nkhani ya ukwati yomwe ndi mbali yofunika kwambiri ndipo imakambidwa ndi mtumiki wa Mboni za Yehova. Nkhaniyi imalimbikitsa okwatiranawo kudziwa mmene Baibulo lingawathandizire kuti azikondana kwambiri, azisangalala komanso zimene angachite kuti banja lawo likhale lolimba.—Aefeso 5:33.

M’mayiko ambiri, boma limapereka chilolezo choti atumiki a Mboni za Yehova azilumbiritsa mkwati ndi mkwatibwi pa ukwati wawo ndipo amachita zimenezo chakumapeto kwa nkhani ya ukwati. Pambuyo polumbira amavekana mphete. Kenako mtumikiyo amalengeza kuti awiriwo ndi mwamuna komanso mkazi okwatirana mwalamulo.

M’mayiko ena, mkazi ndi mwamuna amafunika kukachitira malumbiro awo kumaofesi a boma. Okwatiranawo amachita zimenezi pakangotsala nthawi yochepa kuti nkhani ya ukwati wawo idzakambidwe. Ngati mkwati ndi mkwatibwi sanachite malumbiro awo ku boma, amalumbira kumapeto kwa nkhani ya ukwati. Ngati analumbira kale, angasankhe kubwerezanso koma amalankhula zimenezi mosonyeza kuti anatengana kale. Kumapeto kwa nkhaniyo, amapereka pemphero lopempha Mulungu kuti adalitse banja latsopanolo.

 Kodi maukwati a Mboni za Yehova amachitikira kuti?

A Mboni ambiri amasankha kuti ukwati wawo udzachitikire ku Nyumba ya Ufumu ngati ilipo m’dera lawo. b Kenako amakachitira phwando la ukwati kumalo ena amene anasankha.

 Ndi anthu ati amene angapezekeko?

Ngati ukwatiwo ukuchitikira ku Nyumba ya Ufumu, nthawi zambiri aliyense amaloledwa kupezekapo ngakhalenso anthu omwe si Mboni. Mkwati ndi mkwatibwi ndi amene amasankha anthu oti adzapezeke paphwando la ukwati wawo ngati atasankha kudzachita phwando.

 Nanga alendo ayenera kuvala zotani?

Palibe lamulo la zovala zimene anthu ayenera kuvala ku Nyumba ya Ufumu. Komabe, a Mboni za Yehova amayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo ndipo amayesetsa kuvala bwino komanso mosatayirira posonyeza kuti akulemekeza mwambo wofunika umenewu. Zimakhala bwino kwambiri anthu enanso akatsatira mfundo zimenezi. (1 Timoteyo 2:9) Ngati okwatiranawo asankha kuchita phwando, anthu onse amayenera kuvala mogwirizana ndi mfundo zomwezi.

 Kodi pamakhala kupereka mphatso?

Baibulo limatilimbikitsa kuti tizipereka mosaumira. (Salimo 37:21) A Mboni za Yehova amasangalala kupereka mwa kufuna kwawo ndiponso kulandira mphatso za ukwati. (Luka 6:38) Komabe, a Mboni sapempha kuti apatsidwe mphatso kapenanso kulengeza mayina a anthu omwe apereka mphatso. (Mateyu 6:3, 4; 2 Akorinto 9:7; 1 Petulo 3:8) Kupempha mphatso kapena kulengeza mayina a anthu omwe apereka mphatso n’kosemphana ndi Malemba komanso kungachititse manyazi anthu omwe abwera paukwatipo.

 Kodi pamakhala mwambo wowombanitsa mabotolo a zakumwa?

Ayi. A Mboni za Yehova sachita nawo mwambo wowombanitsa matambula chifukwa choti mwambowu unachokera ku zikhulupiriro zabodza zachipembedzo. c A Mboni amapereka mafuno abwino kwa banja latsopanolo koma sachita zimenezi powombanitsa mabotolo.

 Kodi alendo amawaza mpunga kapena maluwa kwa mkwati ndi mkwatibwi?

Ayi. M’madera ena, anthu amawaza mkwati ndi mkwatibwi mpunga, maluwa kapena zinthu zina. Anthuwa amachita zimenezi chifukwa amakhulupirira kuti zimathandiza anthu okwatiranawo kukhala ndi moyo wautali, banja lawo liziyenda bwino ndiponso kuti azikhala mosangalala. Koma a Mboni za Yehova amapewa kuchita zinthu zokhudzana ndi zikhulupiriro zabodza. Iwo safuniranso ena mwayi chifukwa kuchita zimenezi n’kosemphana ndi zimene Baibulo limanena.—Yesaya 65:11.

 Kodi pamakhala zakudya ndi zakumwa?

Ku Nyumba ya Ufumu sikukhala kudya kapena kumwa. Ena angasankhe kupanga phwando la ukwati wawo pambuyo pake ndipo kuphwandoko kumakhala zakudya kapena zakumwa. (Mlaliki 9:7) Ngati asankha kuti pakhale mowa, amaonetsetsa kuti usakhale wochuluka komanso amaupereka kwa anthu okhawo omwe anafika pamsinkhu wovomerezeka mwalamulo.—Luka 21:34; Aroma 13:1, 13.

 Kodi pamakhala nyimbo komanso kuvina?

Ngati asankha kuchita phwando la ukwati, pamaikidwa nyimbo ndipo anthu amavina. (Mlaliki 3:4) Amasankha nyimbo zabwino potengera zimene amakonda komanso chikhalidwe chawo ndipo amaonetsetsa kuti ndi zoti alendo omwe abwera angasangalale nazo. Ku Nyumba ya Ufumu kumakhalanso nyimbo zokhala ndi uthenga wochokera m’Malemba.

 Kodi a Mboni za Yehova amakondwerera tsiku lawo la ukwati?

Popeza kuti Baibulo silivomereza kapena kuletsa anthu kukondwerera tsiku la ukwati wawo, mabanja a Mboni amasankha okha kukondwerera tsiku la ukwati wawo kapena ayi. Akasankha kukondwerera tsikuli, angaitane achibale, anzawo kapena akhoza kuchita zimenezi paokha.

a Zochitika pamwambowu zikhoza kusiyanasiyana potengera chikhalidwe ndiponso malamulo a kudera komwe kukuchitikira ukwatiwo.

b Mtumiki yemwe amakamba nkhani ya ukwati salandira ndalama iliyonse komanso okwatirana salipira ndalama iliyonse kuti achitire ukwati wawo ku Nyumba ya Ufumu.

c Kuti muone nkhani yosonyeza kuti mwambo wowombanitsa mabotolo unachokera ku zipembedzo zonyenga, werengani mutu wakuti “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 2007.