Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 67

“Lalikira Mawu”

“Lalikira Mawu”

(2 Timoteyo 4:2)

  1. 1. Mulungu watilamula

    Ndipo tikufunika kumvera.

    Tizifotokozera anthu

    Adziwe chiyembekezo chathu.

    (KOLASI)

    Lalikira,

    Indetu onse amve.

    Lalika

    Dzikoli lisanathe.

    Lalika

    Ofatsa amvetsere

    Lalika

    M’dziko lonse.

  2. 2. Mavuto adzatiyesa.

    Tingapezeke tikunyozedwa.

    Kulalikira kungavute.

    Tidzakhulupirirabe M’lungu.

    (KOLASI)

    Lalikira,

    Indetu onse amve.

    Lalika

    Dzikoli lisanathe.

    Lalika

    Ofatsa amvetsere

    Lalika

    M’dziko lonse.

  3. 3. Nthawi zina tizipeza

    Anthu ofuna kutimvetsera.

    Tiziwaphunzitsa mwakhama.

    Tiyeretse dzina la Yehova.

    (KOLASI)

    Lalikira,

    Indetu onse amve.

    Lalika

    Dzikoli lisanathe.

    Lalika

    Ofatsa amvetsere

    Lalika

    M’dziko lonse.