Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 64

Tizigwira Ntchito Yokolola Mosangalala

Tizigwira Ntchito Yokolola Mosangalala

(Mateyu 13:​1-23)

  1. 1 .Tili munthawi yokolola,

    Ndi nthawidi yapadera.

    M’mundamo tirigu wachamo

    Tiyeni tikakolole.

    Yesu akutitsogolera,

    Ndi chitsanzodi chabwino.

    Ndi mwayi wapadera kwambiri

    Kugwira nawo ntchitoyi.

  2. 2. Timakonda M’lungu ndi anthu

    Choncho timachita khama.

    Tiphunzitse anthu mwachangu,

    Mapeto ayandikira.

    Yehova amatidalitsa,

    Timakhala ndi chimwemwe.

    Tipirire pogwira ntchitoyi

    M’lungu adzatithandiza.