Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 60

Akamvera Adzapeza Moyo

Akamvera Adzapeza Moyo

(Ezekieli 3:​17-​19)

  1. 1. Mulungu akufuna

    Tichenjeze anthu

    Kuti tsiku la mkwiyo

    Wake likubwera.

    (KOLASI)

    Akamvera adzapeza

    Inde moyo wosatha.

    Nafe tidzapulumuka

    Tikafalitsa uthenga,

    Uthenga.

  2. 2. Tili ndi uthenga

    Woti tiuze anthu.

    Tiitane anthu abwere

    Kwa Mulungu.

    (KOLASI)

    Akamvera adzapeza

    Inde moyo wosatha.

    Nafe tidzapulumuka

    Tikafalitsa uthenga,

    Uthenga.

    (VESI LOKOMETSERA)

    Mwamsanga tilengeze,

    Anthu amve, aphunzire.

    Adziwe choonadi

    Kuti adzapeze moyo.

    (KOLASI)

    Akamvera adzapeza

    Inde moyo wosatha.

    Nafe tidzapulumuka

    Tikafalitsa uthenga,

    Uthenga.