Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 57

Tizilalikira Anthu a Mitundu Yonse

Tizilalikira Anthu a Mitundu Yonse

(1 Timoteyo 2:4)

  1. 1. Timutsanzire Mulungu wathu

    Pokhala anthu opanda tsankho.

    Akufuna kuti anthu onse

    Amve uthenga, apulumuke.

    (KOLASI)

    Wofunika ndi munthu

    Osati mtundu wake.

    Tiphunzitse onse mosasankha.

    Timakondatu anthu,

    Tiwauze uthenga

    Akhale anzake a Yehova.

  2. 2. Kulikonse angapezekeko

    Kaya akuoneka motani,

    Mtima wawo ndiwo wofunika.

    Yehova amaona mtimawo.

    (KOLASI)

    Wofunika ndi munthu

    Osati mtundu wake.

    Tiphunzitse onse mosasankha.

    Timakondatu anthu,

    Tiwauze uthenga

    Akhale anzake a Yehova.

  3. 3. Yehova amalandira anthu

    Omwe asankha kum’tumikira.

    Choncho anthu a mitundu yonse,

    Tiwauze uthenga wabwino.

    (KOLASI)

    Wofunika ndi munthu

    Osati mtundu wake.

    Tiphunzitse onse mosasankha.

    Timakondatu anthu,

    Tiwauze uthenga

    Akhale anzake a Yehova.