Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 49

Tizisangalatsa Mtima wa Yehova

Tizisangalatsa Mtima wa Yehova

(Miyambo 27:11)

  1. 1. M’lungu takulonjezani

    Kuchita zofuna zanu.

    Tizigwira ntchito yanu,

    Tizikusangalatsani.

  2. 2. Kapolo wanu wanzeru

    Amalengeza za inu.

    Amatipatsa chakudya

    Kuti tizikumverani.

  3. 3. Mutipatse mzimu wanu

    Kuti tikhulupirike

    Ndipo makhalidwe athu

    Azikusangalatsani.