Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 42

Pemphero la Mtumiki wa Mulungu

Pemphero la Mtumiki wa Mulungu

(Aefeso 6:18)

  1. 1. M’lungu Atate Wamphamvuyonse,

    Dzina lanu liziyeretsedwadi.

    Mumachita zomwe mwafuna.

    Tikupempha Ufumu ubwere.

    Pa nthawi yanu M’lungu

    Mudzatidalitsatu.

  2. 2. Mumatipatsa zinthu zabwino,

    Mphatso zoti sitikanazipeza.

    Mumatipatsatu kuwala

    Ndipo mumatipatsanso nzeru.

    Tikukuthokozani

    Ndinudi wachikondi.

  3. 3. Mavuto ndi ambiri m’dzikoli.

    Tikupempha muzititonthozabe.

    Tikuuzeni nkhawa zathu,

    Muzitithandiza kupirira

    Komanso kukwanitsa

    Zomwe tinalonjeza.