Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 37

Kutumikira Yehova Ndi Moyo Wonse

Kutumikira Yehova Ndi Moyo Wonse

(Mateyu 22:37)

  1. 1. Yehova Wamphamvuyonse

    Ineyo ndimakukondani.

    Ndikufuna n’kutumikireni

    Ndi mtima wanga wonse.

    Ndizimvera mawu anu ndi

    Kuchita zofuna zanu.

    (KOLASI)

    Inu Yehova ndinu woyenera

    Kutumikiridwa.

  2. 2. Atate zomwe munalenga

    Zimakulemekezani.

    Ndidzalengeza za inu

    Kwa ena mokhulupirika.

    Yehova muzindithandiza

    Kuti ndikhulupirike.

    (KOLASI)

    Inu Yehova ndinu woyenera

    Kutumikiridwa.