Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 25

Chuma Chapadera

Chuma Chapadera

(1 Petulo 2:9)

  1. 1. Odzozedwa ndi mtundu

    Watsopano wa M’lungu.

    Iye anawagula

    Padziko lapansi.

    (KOLASI)

    Anthu odzozedwa

    Ndi chuma chapadera.

    Amakukondani.

    Amalalikira za inu.

  2. 2. Ndi mtundu wapadera,

    Wokonda choonadi.

    M’lungu wawalandira

    Mu kuwala kwake.

    (KOLASI)

    Anthu odzozedwa

    Ndi chuma chapadera.

    Amakukondani.

    Amalalikira za inu.

  3. 3. Amasonkhanitsanso

    Nkhosa zina mwakhama.

    Ndi okhulupirika

    Kwa Mwanawankhosa.

    (KOLASI)

    Anthu odzozedwa

    Ndi chuma chapadera.

    Amakukondani.

    Amalalikira za inu.