Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 23

Yehova Wayamba Kulamulira

Yehova Wayamba Kulamulira

(Chivumbulutso 11:15)

  1. 1. Ufumu wa Mulungu

    ukulamuliradi.

    Khristu ndiye mwala mu Ziyoni.

    Tonse tikweze mawu,

    tiimbire Mulungu.

    Yesu wakhala pa

    Mpando wachifumu.

    (KOLASI)

    Ufumu ubweretsa chani?

    Chilungamo, choonadi.

    Udzabweretsanso chiyani?

    Moyo wosatha padziko.

    Tamandani Yesu Mfumu,

    Iye ndi wachikondi.

  2. 2. Khristu ali pampando.

    Amagedo ifika

    Kudzawononga anthu oipa.

    Choncho tilalikire

    kuti ambiri amve

    Ndipo ofatsa abwere

    kwa Mulungu.

    (KOLASI)

    Ufumu ubweretsa chani?

    Chilungamo, choonadi.

    Udzabweretsanso chiyani?

    Moyo wosatha padziko.

    Tamandani Yesu Mfumu,

    Iye ndi wachikondi.

  3. 3. Tilemekeze Mfumu

    yomwe ndi yachikondi.

    Yatumidwa ndi Yehova M’lungu.

    Tizipempha Yehova

    kuti atithandize,

    Chifukwa oipa

    adzawonongedwa.

    (KOLASI)

    Ufumu ubweretsa chani?

    Chilungamo, choonadi.

    Udzabweretsanso chiyani?

    Moyo wosatha padziko.

    Tamandani Yesu Mfumu,

    Iye ndi wachikondi.