Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 16

Tamandani Yehova Chifukwa cha Mwana Wake Wodzozedwa

Tamandani Yehova Chifukwa cha Mwana Wake Wodzozedwa

(Chivumbulutso 21:2)

  1. 1. M’lungu anadzoza Yesu

    Kukhala Mfumu yathu

    Kuti chifuniro cha M’lungu

    Chichitike padzikoli.

    (KOLASI)

    Tamandani Yehova M’lungu

    Chifukwa cha wodzozedwa.

    Inu nkhosa zokhulupirika

    Zomvera malamulo,

    Tamandani wodzozedwayo

    Wolamulira kumwamba,

    Amene amalemekezetsa

    Dzina la M’lungu wathu.

  2. 2. Abale a Yesu Khristu

    Osankhidwa ndi M’lungu,

    Adzalamulira ndi Yesu.

    Adzayeretsa dzikoli.

    (KOLASI)

    Tamandani Yehova M’lungu

    Chifukwa cha wodzozedwa.

    Inu nkhosa zokhulupirika

    Zomvera malamulo,

    Tamandani wodzozedwayo

    Wolamulira kumwamba,

    Amene amalemekezetsa

    Dzina la M’lungu wathu.