Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 150

Bwerani kwa Mulungu Kuti Mupulumuke

Bwerani kwa Mulungu Kuti Mupulumuke

(Zefaniya 2:3)

  1. 1. Mitundu ya anthu

    Ikutsutsabe Yesu.

    Ulamuliro wa anthu

    Utha watero M’lungu.

    Ufumu wa M’lungu

    Ukulamuliradi.

    Yesu adzachotsa adani.

    Adzatha posachedwa.

    (KOLASI)

    Bweranitu kwa Yehova

    Kuti mudzapulumuke.

    Musakayike,

    Muzimumvera,

    Mukhale kumbali yake.

    Adzakupulumutsani

    Ndi mphamvu zake.

  2. 2. Anthu akusankha

    Kumvetsera uthenga.

    Timalalikira onse.

    Enatu amakana.

    Tikamavutika

    Tisakhale ndi mantha.

    M’lungu adzatisamalira

    Timukhulupirire.

    (KOLASI)

    Bweranitu kwa Yehova

    Kuti mudzapulumuke.

    Musakayike,

    Muzimumvera,

    Mukhale kumbali yake.

    Adzakupulumutsani

    Ndi mphamvu zake.