Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 132

Tsopano Ndife Thupi Limodzi

Tsopano Ndife Thupi Limodzi

(Genesis 2:​23, 24)

  1. 1. Fupa la mafupa anga,

    Ndiwe mnofu wa mnofu wanga.

    M’lungu wandipatsa mnzanga,

    Pano ndiwe wanga

    Ndife thupi limodzidi.

    Tizilandira madalitso.

    Monga mwamuna ndi mkazi

    Pano ndife banja.

    Tizitumikira Yehova.

    Tsiku ndi tsiku

    Tikulitse chikondi.

    Zimene talumbirazi

    Tizichita kwa moyo wonse.

    Tizilemekeza M’lungu

    Ndipo ukhalebe wanga.