Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 115

Tizithokoza Kuleza Mtima kwa Mulungu

Tizithokoza Kuleza Mtima kwa Mulungu

(2 Petulo 3:15)

  1. 1. Yehova Mulungu wamphamvu

    Mumakonda chilungamo.

    Ngakhale zoipa m’dziko

    Zikungochulukirabe,

    Tikudziwa simukuchedwa

    Posachedwa mudzazichotsa.

    (KOLASI)

    Tikudikira mwachidwi.

    Timatamanda dzina lanu.

  2. 2. Zaka zambiritu kwa inu

    Ndi nthawi yochepa chabe.

    Tsiku lanu lalikulu

    Layandikira kwambiri.

    Anthu ochimwa akalapa

    Mumasangalala kwambiri.

    (KOLASI)

    Tikudikira mwachidwi.

    Timatamanda dzina lanu.