Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mungatani Kuti Musayambe Kumwa Mowa Mopitirira Malire?

Mungatani Kuti Musayambe Kumwa Mowa Mopitirira Malire?

Anthu ena amayamba kumwa mowa mopitirira malire akakhala kuti ali ndi nkhawa, ali okhaokha kapenanso akangoboweka. Kodi pano mwayamba kumwa kwambiri kuposa mmene munkamwera? Ngati zili choncho, mungatani kuti mupewe kumwa mowa kwambiri kapenanso kuti musafike pomangokhalira kumwa mowa? Mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni kuti musamamwe mowa mopitirira malire.

 Kodi munthu angadziwe bwanji kuti samwa mowa mopitirira malire?

Zimene Baibulo limanena: “Usakhale pakati pa anthu omwa vinyo kwambiri.”—Miyambo 23:20.

Ganizirani izi: Baibulo silimaletsa kumwa mowa mosapitirira malire. (Mlaliki 9:7) Komabe limasonyeza kuti pali kusiyana pakati pa kumwa mowa mosapitirira malire ndi kuledzera komanso uchidakwa. (Luka 21:34; Aefeso 5:18; Tito 2:3) Ngakhale kuti munthu asafike pokhala chidakwa, koma kumwa mowa kwambiri kungachititse kuti asamasankhe zinthu mwanzeru, kungawononge thanzi lake, kapenanso kungasokoneze ubwenzi wake ndi anthu ena.—Miyambo 23:29, 30.

Akatswiri ambiri amanena kuti pali kusiyana pakati pa kumwa mowa mosapitirira malire ndi kumwa mowa kwambiri. Nthawi zambiri amayeza kuchuluka kwa mowa umene munthu amamwa patsiku komanso pa mlungu potengera mlingo woyenerera womwera mowa. a Komabe, anthu akamwa mowa amachita zinthu m’njira zosiyanasiyana potengera ndi mmene thupi lawo liliri. Ndipo ena amasankha kusiyiratu kumwa mowa. Bungwe Loona Zaumoyo Padziko Lonse linanena izi:

“Nthawi zina ngakhale kungomwa botolo kapena tambula imodzi kapena awiri kukhoza kukhala koopsa—Mwachitsanzo:

  • Poyendetsa galimoto kapena kugwiritsa ntchito mashini.

  • Ukakhala woyembekezera kapena woyamwitsa.

  • Ukamamwa mankhwala enaake.

  • Ngati ukudwala matenda enaake.

  • Ngati simutha kudziletsa mukayamba kumwa.”

 Zizindikiro zosonyeza kuti munthu wayamba kumwa mowa mopitirira malire

Zimene Baibulo limanena: “Tiyeni tifufuze njira zathu kuti tizidziwe.”—Maliro 3:40.

Ganizirani izi: Mungathe kupewa mavuto amene amabwera chifukwa chakumwa mowa mopitirira malire ngati mutamadzifufuza nthawi ndi nthawi n’kusintha ngati pakufunika kutero. Zizindikiro zotsatirazi zingasonyeze kuti mwayamba kumwa mopitirira malire.

  • Mumadalira mowa kuti musangalale. Mumaona kuti popanda kumwa mowa simungathe kumasuka, kucheza ndi anzanu kapena kusangalala. Komanso mumamwa mowa kuti muiwale mavuto anu.

  • Mwayamba kumwa kwambiri kuposa kale. Mukumamwa pafupipafupi, mowa wake ukumakhala wamphamvu kwambiri, komanso mukumafunika kumwa mowa wambiri kuposa kale kuti mumve bwino.

  • Kumwa mowa kwayambitsa mavuto kunyumba kapena kuntchito. Mwachitsanzo, mukumaononga ndalama zambiri kugulira mowa kuposa ndalama zimene mungakwanitse.

  • Mukamwa mowa mumachita zinthu zoika moyo wanu pangozi. Mwachitsanzo, kuyamba kuyendetsa galimoto, kusambira kapena kugwiritsa ntchito mashini.

  • Anthu ena akumadandaula ndi mmene mukumwera mowa. Akakuuzani mukumadziikira kumbuyo. Mumayesetsa kubisa kapena kunama kuti anthu asadziwe mmene mukumwera.

  • Mukuvutika kusiya. Mwayeserapo kuti muchepetse kapena musiye kumwa mowa koma mukulephera.

 Mfundo 5 zimene zingakuthandizeni kuti muzidziikira malire.

1. Khalani ndi zolinga.

Zimene Baibulo limanena: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira.”—Miyambo 21:5.

Yesani izi: Sankhani masiku amene muzimwa pamlungu. Sankhani mlingo wabwino wa mowa umene muzimwa pa masiku amenewa. Kenako sankhani masiku awiri kapena kuposerapo pamlungu amene simuzimwa mowa.

Bungwe lina la ku U.K, lothandiza anthu pa nkhani ya mowa linati: “Kukhala masiku ena osamwa kumathandiza kuti munthu apewe chizolowezi chomangokhalira kumwa mowa.”

2. Yesetsani kukwaniritsa zolinga zanu.

Zimene Baibulo limanena: ‘Malizitsani zimene munayamba.’—2 Akorinto 8:11.

Yesani izi: Muzisamala popungula mowa woti mumwe kuti usachuluke kwambiri. Komanso muziyang’ana kuchuluka kwa maperesenti a mowa womwe mukufuna kumwa n’cholinga choti mudziwe mphamvu yake.

Bungwe lina la ku United States linati: “Kusintha zinthu zing’onozing’ono kungakuthandizeni kuti mupewe mavuto aakulu amene angathe kubwera chifukwa chomwa mowa mopitirira muyezo.”—U.S. National Institute on Alcohol Abuse and Alcoholism.

3. Musamasinthe zimene mwasankha.

Zimene Baibulo limanena: “Mukati Inde akhaledi Inde ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi.”—Yakobo 5:12.

Yesani izi: Khalani okonzeka kunena kuti “Ayi” mwaulemu koma momveka bwino ngati munthu wina atakupatsani mowa umene ungasokoneze zolinga zanu.

Bungwe la ku United States lija linanenanso kuti, “mukafulumira kukana munthu wina akamakupatsani mowa zidzakuthandizani kuti musakopeke.”

4. Muziganizira ubwino wa zimene mwasankha.

Zimene Baibulo limanena: “Mapeto a chinthu amakhala bwino kuposa chiyambi chake.”—Mlaliki 7:8.

Yesani izi: Lembani zifukwa zimene mukufunira kuti musamamwe mowa mopitirira malire. Mukhoza kulemba zinthu ngati kugona mokwanira, kukhala ndi thanzi labwino, kusamala ndalama ndiponso kukhala bwino ndi anthu. Mukamauza anthu ena zimene mwasankha muzinena kwambiri za ubwino wake osati mavuto amene mukumane nawo.

5. Muzipemphera kwa Mulungu kuti akuthandizeni.

Zimene Baibulo limanena: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”—Afilipi 4:13.

Yesani izi: Ngati mukuda nkhawa chifukwa cha mmene mumamwera mowa, pempherani kwa Mulungu kuti akuthandizeni. M’pempheni kuti akupatseni mphamvu komanso akuthandizeni kukhala wodziletsa. b Ndipo muzipeza nthawi yofufuza nzeru zothandiza zimene zimapezeka m’Mawu ake Baibulo. Mulungu adzakuthandizani kuti muthane ndi vuto lomwa mowa mopitirira malire.

a Dipatimenti Yoona za Umoyo wa Anthu ku United States imanena kuti kumwa mowa mopitirira malire kumatanthauza “kumwa mabotolo kapena matambula 4 patsiku kapenanso mabotolo mwinanso matambula 8 pa mlungu kwa azimayi ndiponso kumwa mabotolo kapena matambula 5 patsiku mwinanso kumwa mabotolo kapena matambula 15 pa mlungu kwa azibambo.” Malamulo okhudza kamwedwe ka mowa amasiyana dziko lililonse. Kuti mudziwe mlingo woyenerera womwera mowa wa inuyo, funsani azaumoyo.

b Ngati zikukuvutani kuchepetsa mmene mumamwera mowa mukhoza kupempha akatswiri kuti akuthandizeni.