Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?

Kupereka Chithandizo Padziko Lonse pa Nthawi ya Mliri

Kupereka Chithandizo Padziko Lonse pa Nthawi ya Mliri

JULY 1, 2021

 M’mwezi wa March 2020, Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse linalengeza kuti COVID-19 ndi mliri wapadziko lonse. Pa nthawiyo, ambirife sitikanaganiza kuti mliriwu udzakhala ukufalikirabe mpaka patapita chaka chathunthu. Anthu mamiliyoni angapo kuphatikizapo a Mboni za Yehova ambiri, akhudzidwa ndi mliriwu kaya chifukwa cha kudwala, kuvutika maganizo kapena kukumana ndi mavuto azachuma. Kodi a Mboni za Yehova achita zotani kuti apereke chithandizo pa nthawi yovutayi?

Kupereka Chithandizo kwa Anthu Amene Akufunikira

 Komiti ya Ogwirizanitsa ya Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova inakonza kuti Makomiti Othandiza Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi 950 apangidwe padziko lonse chifukwa cha mliri wa COVID-19. Makomitiwa apereka chithandizo kwa a Mboni m’madera awo kapena kukonza kuti a Mboniwo athandizidwe ndi boma. Makomitiwa akonzanso kuti apereke chithandizo m’madera osiyanasiyana.

 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitika ku Paraguay. Nyuzipepala ina inanena kuti mliriwu wachititsa kuti “anthu ambiri ku Paraguay avutike ndi njala.” Koma Komiti Yothandiza Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi m’dzikoli inali itayamba kale kupereka makatoni a chithandizo kwa anthu. Katoni iliyonse inali ndi chakudya, zinthu zogwiritsira ntchito poyeretsa komanso zinthu zina zofunika. Zinthuzi zinali zokwanira kuti zithandize banja la anthu 4 kwa milungu iwiri ndipo mtengo wake unali wa ndalama zokwana madola 30 a ku United States.

 Kodi anthu ogwira ntchito m’makomitiwa amachita chiyani kuti azidziteteza komanso kuteteza anthu ena kuti asadwale COVID-19? Mwachitsanzo iwo amavala mamasiki komanso amakhala motalikirana ndi anthu ena. Amaonetsetsanso kuti makampani amene akuwagula zakudya akutsatira malangizo okhudza ukhondo komanso kudzitetezera kumatenda pokonza chakudyacho. Mwachitsanzo, amatsimikizira kuti onse amene amanyamula makatoniwo amavala zodzitetezera ku matenda, amayeretsa n’kuthira mankhwala opha majeremusi m’magalimoto awo komanso pamalo amene amasungira makatoniwo. Nawonso anthu amene amakapereka makatoniwo amakhala motalikirana ndi abale amene akuwalandira.

Kugwiritsa Ntchito Zopereka Mwanzeru

 Pofika mu January 2021, Komiti ya Ogwirizanitsa inali itavomereza kuti ndalama zokwana madola 25 miliyoni a ku United States zigwiritsidwe ntchito popereka chithandizo chifukwa cha mliri wa COVID-19. Abale a ku Nthambi komanso a m’makomitiwo amagwiritsa ntchito ndalamazi mosamala kwambiri komanso amayesetsa kugula zinthu pa mtengo wabwino. Mwachitsanzo, ku Chile abale oyendetsa ntchito yokapereka chithandizo ankafuna kugula mphodza zokwana makilogalamu 750 kwa wamalonda wina. Koma mtengo wa mphodza unali utakwera kuwirikiza kawiri m’mwezi umodzi wokha. Ndiye patapita maola awiri atavomera kuti agule mphodzazo pa mtengo wokwerawo, wamalondayo anawauza kuti munthu wina anali atangobweza kumene mphodza zimene anagula. Choncho m’malo mogulitsa mphodzazo pa mtengo wokwera, wamalondayo anawauza kuti awagulitsa pa mtengo wa mwezi wapitawo.

 Koma pamene abalewo anapita kukatenga mphodzazo, wamalondayo anakana kuwapatsa pa mtengo umene anagwirizana. Iye ananena kuti anachita zimenezo chifukwa abalewo sankapereka chakudya mwachilungamo koma ankakondera mofanana mabungwe ena. M’bale wina anapemphera mwachidule chamumtima, kenako anauza wamalondayu kuti abale anali atafufuza bwinobwino m’mipingo kuti adziwe anthu amene akufunikiradi chithandizo. Abalewa anafotokozanso kuti anthu olandira chithandizo ndi azikhalidwe zosiyanasiyana choncho amaika zinthu m’makatoniwo mogwirizana ndi zimene banja lililonse lingafunikire. Kenako anauza wamalondayo kuti ndalama zonse zimene anthu amapereka kwa a Mboni za Yehova komanso ntchito imene a Mboni amagwira popereka chithandizocho amazichita mwa kufuna kwawo. Iye anadabwa ndipo anavomera kugulitsa mphodzazo pa mtengo wotsika uja komanso nthawi ina anawonjezera kwaulere makilogalamu 400 a mphodza pa oda imene abale anapereka.

“Umboni Woti Ali ndi Chikondi Chenicheni”

 Mkazi wamasiye wina ku Liberia dzina lake Lusu ndi wachikulire ndipo amakhala ndi achibale 5. Ndiye tsiku lina m’mawa akudya n’kumakambirana lemba la tsiku, mdzukulu wa Lusu wazaka 7 anaona kuti chakudya chonse chatha panyumbapo. Ndiyeno anafunsa kuti, “Ndiye kaya tidya chiyani?” Lusu anamuuza kuti anali atapemphera kale kwa Yehova kuti awathandize ndipo anali ndi chikhulupiriro choti awasamalira. Tsiku lomwelo masana, akulu mumpingo anamuimbira foni Lusu n’kumuuza kuti abwere kudzatenga chithandizo cha chakudya. Lusu anati: “Mdzukulu wanga ananena kuti panopa amadziwa kuti Yehova amamva ndi kuyankha mapemphero chifukwa wayankha pemphero langa.”

Ana a ku Democratic Republic of Congo anajambula zithunzi pothokoza abale chifukwa cha chithandizo cha chakudya

 Mayi wina ku Democaratic Republic of Congo amakhala moyandikana ndi banja lina la Mboni. Ataona banjali likulandira chakudya kuchokera kwa a Mboni anzawo, anati, “Mliriwu ukatha tidzakhala a Mboni za Yehova chifukwa iwo akhala akusamalira abale ndi alongo awo pa nthawi yovutayi.” Mwamuna wake anamufunsa kuti, “Ndiye ukhala wa Mboni za Yehova kuti ungolandira thumba la mpunga basi?” Mayiyo anayankha kuti, “Ayi, koma thumba la mpungalo ndi umboni woti ali ndi chikondi chenicheni.”

 A Mboni za Yehova akwanitsa kuthandiza abale ndi alongo awo mwamsanga pa nthawi ya mliriyi chifukwa choti inuyo mwapereka ndalama mosaumira. Zikomo kwambiri chifukwa cha zimene mwapereka pogwiritsa ntchito njira zofotokozedwa pa donate.isa4310.com.