Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

N’chifukwa chiyani m’Baibulo mumapezeka maulosi?

N’chifukwa chiyani Baibulo linafotokoza zinthu zomwe zikuchitika masiku ano?—Luka 21:10, 11.

M’Baibulo muli maulosi ambiri onena mwatsatanetsatane zimene zidzachitike m’tsogolo. Palibe munthu amene angafotokoze zinthu zam’tsogolo ngati mmene Baibulo limachitira. Choncho kukwaniritsidwa kwa maulosi amenewa kumatitsimikizira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu.—Werengani Yoswa 23:14; 2 Petulo 1:20, 21.

Maulosi amene anakwaniritsidwa kale amatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri Mulungu. (Aheberi 11:1) Amatitsimikiziranso kuti zimene Mulungu analonjeza zoti dzikoli lidzakhala paradaiso zidzakwaniritsidwa. Zimenezi zimatithandiza kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba.—Werengani Salimo 37:29; Aroma 15:4.

Kodi maulosi a m’Baibulo amatithandiza bwanji?

Maulosi ena amanenedwa n’cholinga chothandiza atumiki a Mulungu kudziwa zochita, ulosiwo ukamadzakwaniritsidwa. Mwachitsanzo, Akhristu oyambirira ataona zinthu zina zimene ulosi unanena zikuchitika, anathawa mu Yerusalemu. Ndiyeno pamene mzindawu unkawonongedwa chifukwa choti anthu ambiri anakana kukhulupirira Yesu, Akhristu omwe anathawa aja anapulumuka.—Werengani Luka 21:20-22.

Maulosi amene akukwaniritsidwa masiku ano amatitsimikizira kuti posachedwapa, Ufumu wa Mulungu uwononga maboma onse a anthu. (Danieli 2:44; Luka 21:31) Choncho m’pofunika kuti aliyense azichita zinthu zosonyeza kuti ali kumbali ya Yesu Khristu, amene anasankhidwa ndi Mulungu kuti akhale Mfumu.—Werengani Luka 21:34-36.