Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI TIMAFUNIKIRADI MULUNGU?

N’chifukwa Chiyani Timafunikira Mulungu?

N’chifukwa Chiyani Timafunikira Mulungu?

Akatswiri a maganizo amati anthufe timafunika zinthu zauzimu kuti tikhaledi osangalala. Umboni wa zimenezi ndi woti anthu amafuna kumamvera winawake amene amamuona kuti ndi wamkulu kuposa iwowo. Pofuna kukwaniritsa zimenezi, ambiri amathera nthawi yawo akusangalala ndi zachilengedwe, kupanga zinthu, kuimba ndi zina zotero. Komabe ambiri amaona kuti zinthu zimenezi siziwathandiza kwenikweni kuti akhale osangalala.

Mulungu amafuna kuti anthufe tikhale ndi moyo wosangalala panopa komanso kosatha

Anthu amene amaphunzira Baibulo sadabwa ndi mfundo yoti anthufe timafunikira zinthu zauzimu. Machaputala oyamba a m’buku la Genesis amasonyeza kuti Mulungu atalenga anthu awiri oyamba, ankalankhula nawo nthawi ndi nthawi ndipo izi zinapangitsa kuti akhale naye pa ubwenzi. (Genesis 3:8-10) Mulungu sanalenge anthu m’njira yoti azichita zinthu paokha osadalira Mulungu. Anthufe timafunika kuti tizilandira malangizo ochokera kwa Mlengi wathu ndipo m’Baibulo muli mavesi ambiri osonyeza zimenezi.

Mwachitsanzo, Yesu ananena kuti: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.” (Mateyu 5:3) Mawu amenewa akutithandiza kuona kuti tingakhale ndi moyo wosangalala ngati titamaphunzira za Mulungu ndi kuchita zimene iye amafuna. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Yankho lake likupezeka m’mawu amene Yesu ananena. Iye anati: “Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.” (Mateyu 4:4) Kodi mawu ochokera pakamwa pa Yehova, kapena kuti malangizo ochokera kwa iye amene ali m’Baibulo, angatithandize bwanji kukhala osangalala? Tiyeni tikambirane njira zitatu.

Timafunikira Malangizo Ochokera kwa Mulungu

Masiku ano pali akatswiri ambiri amene amapereka malangizo pa nkhani ya kupeza mabwenzi, chikondi, moyo wa banja, kuthetsa kusamvana, kukhala osangalala komanso zimene munthu angachite kuti akhale ndi moyo waphindu. Koma kodi pali amene angapereke malangizo othandiza pa nkhani zimenezi kuposa Yehova Mulungu, yemwe ndi Mlengi wathu?

Mofanana ndi buku la malangizo, m’Baibulo muli malangizo oti tiziyendera pa moyo wathu

 Mwachitsanzo, mukagula chinthu chatsopano monga foni kapena wailesi chimakhalanso ndi buku la malangizo lochokera kwa amene anapanga chinthucho, lomwe limafotokoza mmene mungachigwiritsire ntchito bwino. Baibulo lili ngati buku lamalangizo limeneli. Ndi buku lochokera kwa Mulungu, Mlengi wa anthu, limene tiyenera kutsatira malangizo ake. Buku limeneli limatithandiza kudziwa mmene anthufe tinapangidwira komanso zimene tingachite kuti zinthu zizitiyendera bwino.

Mofanana ndi mmene buku lamalangizo limakhalira, Baibulo limatithandiza kudziwa zoyenera kupewa kuti zisativulaze komanso zoyenera kuchita kuti moyo wathu ukhale wabwino. Malangizo amene anthu ena angatipatse angaoneke ngati abwino komanso osavuta kuwatsatira. Koma kodi si zoona kuti malangizo ochokera kwa Mlengi wathu ndi amene angatithandize kukhala ndi moyo wabwino komanso kupewa mavuto?

“Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino, amene ndimakuchititsani kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo. Zingakhale bwino kwambiri mutamvera malamulo anga! Mukatero mtendere wanu udzakhala ngati mtsinje, ndipo chilungamo chanu chidzakhala ngati mafunde a m’nyanja.”—Yesaya 48:17, 18

Baibulo lili ndi malangizo komanso mayankho a mafunso ofunika

Yehova Mulungu satikakamiza kuti tizitsatira malangizo amene amatipatsa. Koma chifukwa chotikonda amatiuza kuti: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino, amene ndimakuchititsani kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo. Zingakhale bwino kwambiri mutamvera malamulo anga! Mukatero mtendere wanu udzakhala ngati mtsinje, ndipo chilungamo chanu chidzakhala ngati mafunde a m’nyanja.” (Yesaya 48:17, 18) Mwachidule tingati, tikamatsatira malangizo a Mulungu tidzakhala ndi moyo wabwino. M’mawu ena tingati, kuti tikhale ndi moyo wabwino, timafunikira Mulungu.

Timafunikira Kudziwa Chifukwa Chake Padzikoli Pali Mavuto

Anthu ena amaona kuti safunikira Mulungu chifukwa amaona kuti padzikoli pali mavuto ambirimbiri ndipo izi zimawavuta kukhulupirira kuti kuli Mulungu wachikondi. Mwachitsanzo, iwo amadzifunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani nawonso anthu abwino amavutika?’ ‘N’chifukwa chiyani ana osalakwa amabadwa olumala?’ ‘N’chifukwa chiyani padzikoli pamachitika zinthu zopanda chilungamo?’ Mafunso amenewa ndi ofunika zedi ndipo kudziwa mayankho ake kungatithandize kwambiri. Koma m’malo mofulumira kuimba mlandu Mulungu chifukwa cha mavutowa, tiyeni tione zimene Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, limatiuza pa nkhani imeneyi.

M’chaputala 3 cha Genesis, muli nkhani yonena za Satana, yemwe pogwiritsa ntchito njoka anapusitsa anthu awiri oyambirira kuti apandukire Mulungu mwa kudya chipatso cha mtengo wodziwitsa zabwino ndi zoipa. Satana anauza Hava kuti: “Kufa simudzafa ayi. Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye chipatso cha mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.”—Genesis 2:16, 17; 3:4, 5.

Apa Satana ananena kuti Mulungu ndi wabodza komanso amalamulira mopanda chilungamo. Tingati anati anthu atamamvera Satanayo zinthu zingamawayendere bwino. Kodi nkhani zimenezi zikanathetsedwa bwanji? Yehova anaona kuti panafunika nthawi kuti onse aone ngati zimene Satana anamunenera zili zoona kapena zabodza. Choncho Mulungu anapereka mwayi kwa Satana ndi amene  ali kumbali yake kuti asonyeze ngati anthu angathe kukhala bwinobwino popanda kulamuliridwa ndi Mulungu.

Kodi inuyo mukuona kuti zimene Satana ananena n’zoona? Kodi anthu angakhale ndi moyo wabwino popanda kulamuliridwa ndi Mulungu? Zinthu monga kupanda chilungamo, matenda, imfa, kuphwanya malamulo, makhalidwe oipa, nkhondo, kupha anthu komanso zoipa zonse zomwe zakhala zikuvutitsa anthu kwa zaka zambirimbiri, ndi umboni wakuti anthu alephera kudzilamulira okha. Baibulo limasonyeza kuti Mulungu si amene amachititsa mavuto amenewa ndipo limatiuza chimene chimachititsa. Limati: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.”—Mlaliki 8:9.

Tikaganizira zimenezi, tingaone kuti anthufe tikufunika kudalira Mulungu, osati kuti angotiuza chifukwa chake padzikoli pali mavuto, koma kuti atithetserenso mavutowa. Kodi Mulungu adzachita chiyani pothetsa mavutowa?

M’pofunika Kuthandizidwa ndi Mulungu

Kwa zaka zambiri anthu akhala akufunitsitsa kuti asamadwale, kukalamba komanso kufa. Ayesa njira zosiyanasiyana kuti zimenezi zitheke koma zawakanika. Ena aganizapo kuti kukhala kudera linalake komanso kumwa mankhwala kapena madzi enaake kungathandize kuti akhale ndi moyo wautali. Koma zonsezi sizinawathandize kwenikweni.

Mulungu amafuna kuti anthufe tizikhala ndi moyo wabwino komanso wosangalala. Chimenechi ndiye chinali cholinga chake polenga anthu, ndipo zimenezi n’zimene adzachitire anthu m’tsogolo. (Genesis 1:27, 28; Yesaya 45:18) Yehova Mulungu amatitsimikizira kuti chilichonse chimene wanena adzachikwaniritsa. (Yesaya 55:10, 11) Baibulo limatiuza kuti Mulungu adzapangitsa kuti dzikoli likhalenso Paradaiso ngati mmene zinalili poyamba. M’buku lomaliza la m’Baibulo muli mawu awa: “ [Yehova Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.” (Chivumbulutso 21:4) Kodi Mulungu adzachita bwanji zimenezi, nanga ifeyo tingapindule bwanji ndi lonjezo limeneli?

Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti chifuniro cha Mulungu chichitike. Anthu ambiri amadziwa bwino pemphero, lomwe ambiri amalitchula kuti Pemphero la Ambuye ndipo ena anachita kuliloweza. Pempheroli limati: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Yehova Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumu wa Mulungu kuchotsa mavuto onse amene ulamuliro wa anthu wayambitsa, n’kubweretsa dziko latsopano lolungama lomwe walonjeza. * (Danieli 2:44; 2 Petulo 3:13) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tidzakhale m’dziko limeneli?

 Yesu ananena zimene tiyenera kuchita. Iye anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.” (Yohane 17:3) Choncho Mulungu angatithandize kudzapeza moyo wosatha m’dziko latsopano. Umenewu ndi umboni winanso wosonyeza kuti anthufe timafunikira Mulungu.

Tiyenera Kudziwa Mulungu

Zaka 2,000 zapitazo, mtumwi Paulo ali pabwalo la Areopagi ku Atene anauza anthu a kumeneko zokhudza Mulungu kuti: “Iyeyo amene amapatsa anthu onse moyo, mpweya, ndi zinthu zonse. Pakuti chifukwa cha iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo, monga mmene andakatulo ena pakati panu anenera kuti, ‘Pakuti ndife mbadwa zake.’”—Machitidwe 17:25, 28.

Zimene Paulo anauza anthu a ku Atene zidakali zoona mpaka pano. Mlengi wathu amatipatsa mpweya umene timapuma, chakudya chimene timadya komanso madzi amene timamwa. Anthufe sitingakhale ndi moyo popanda zinthu zabwino zimene Yehova amatipatsa. Koma kodi n’chifukwa chiyani Mulungu amapitirizabe kupereka kwa anthu zinthu zabwino zimenezi, kaya anthuwo amakhulupirira kuti iye alipo kapena ayi? Paulo ananena kuti Mulungu amachita zimenezi “kuti anthuwo afunefune Mulungu, amufufuzefufuze ndi kumupezadi, ngakhale kuti kwenikweni, iye sali kutali ndi aliyense wa ife.”—Machitidwe 17:27.

Kodi mukufuna kumudziwa bwino Mulungu, kudziwa zambiri zimene walonjeza komanso malangizo amene iye amatipatsa otithandiza kukhala ndi moyo wabwino panopa komanso kosatha? Ngati ndi choncho, funsani munthu amene anakupatsani magaziniyi kapena amene amafalitsa magaziniwa kuti akuthandizeni.

^ ndime 20 Kuti mudziwe zambiri zokhudza zimene Ufumu wa Mulungu udzachite pokwaniritsa cholinga cha Mulungu padziko lapansi, werengani mutu 8 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Mungathenso kuchita dawunilodi bukuli pa webusaiti yathu ya www.isa4310.com.