Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zipembedzo Mungazikhulupirire pa Nkhani ya Makhalidwe Abwino?

Kodi Zipembedzo Mungazikhulupirire pa Nkhani ya Makhalidwe Abwino?

Mtsikana wina yemwe amagwira ntchito zachipatala, dzina lake Sylvia, ananena kuti: “Pakoleji imene ndinkaphunzira panali anthu ambiri amene ankati amakonda kupemphera. Koma zimene ankachita zinali zosiyana kwambiri ndi zimene munthu wokonda kupemphera ayenera kuchita. Ankabera mayeso komanso ankagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo omwe anali oletsedwa.”

Bambo wina, dzina lake Lionel ananena kuti: “Anthu amene ndimagwira nawo ntchito amanama komanso amajomba kuntchito kuti akudwala koma asakudwala. Ngakhale amapita kutchalitchi sagwiritsa ntchito zimene amaphunzira kutchalitchiko.”

Zipembedzo zambiri sizimalimbikitsa anthu kuti azikhala ndi makhalidwe abwino. N’chifukwa chake anthu ambiri masiku ano ali “ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu” koma “amakana kuti mphamvu ya kudziperekako iwasinthe.” (2 Timoteyo 3:5) Atsogoleri azipembedzo zambiri satsatira mfundo za makhalidwe abwino komanso samathandiza nkhosa zawo kuti zizitsatira malangizo a m’Baibulo okhudza makhalidwe abwino. N’chifukwa chake anthu ambiri amaganiza kuti akhoza kuchita makhalidwe aliwonse oipa chifukwa Mulungu alibe nazo ntchito.

KODI BAIBULO LIMATI CHIYANI PA NKHANI YA MAKHALIDWE ABWINO?

Baibulo limasonyeza kuti zimene timachita zimamukhudza Mulungu. Mwachitsanzo, kale kwambiri Mulungu ‘ankakhumudwa’ Aisiraeli akasiya kumvera malamulo ake. (Salimo 78:40) Komabe ‘kumwamba kumakhala chisangalalo’ munthu akalapa moona mtima n’kusiya khalidwe lake loipa. (Luka 15:7) Munthu akazindikira makhalidwe abwino amene Atate wathu wakumwamba ali nawo, amayamba kumukonda kwambiri. Zimenezi zimamuchititsa kuti ayambe kukonda zimene Mulungu amakonda komanso kudana ndi zimene Mulungu amadana nazo.—Amosi 5:15.

KODI A MBONI ZA YEHOVA AMATANI PA NKHANIYI?

Nyuzipepala ina ya ku Salt Lake City ku Utah, m’dziko la United States, inanena kuti a Mboni za Yehova “amalimbikitsa anthu kuti azikondana kwambiri m’mabanja, azithandiza anthu ena komanso kuti akhale nzika zodalirika.” (Deseret News) Nyuzipepalayi inanenanso kuti: “A Mboni za Yehova amayesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino. Amakhulupirira kuti zinthu ngati kusuta fodya, kuledzera, kumwa mankhwala osokoneza bongo, juga, chiwerewere komanso khalidwe logonana amuna kapena akazi okhaokha, zimawonongetsa ubwenzi ndi Mulungu.”

Kodi atsogoleri azipembedzo athandiza nkhosa zawo kukhala ndi makhalidwe abwino amene Mulungu amafuna?

Kodi a Mboni za Yehova amapindula bwanji chifukwa chodziwa makhalidwe a Mulungu? Sylvia yemwe tamutchula kale uja ananena kuti: “Anthu ambiri ogwira ntchito zachipatala amachita zachinyengo ndipo n’zosavuta kutengera makhalidwe amenewo. Koma kudziwa kuti Yehova * amadana ndi zachinyengo kumandithandiza kuti ndizipewa khalidwe limeneli. Panopa ndine wosangalala komanso ndili ndi mtendere wamumtima.” Sylvia amaona kuti kutsatira zimene amaphunzira ku chipembedzo chake kwamuthandiza kuti akhale ndi moyo wabwino.

^ ndime 9 Baibulo limanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova.