Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

N’chifukwa chiyani padzikoli palibe mtendere weniweni?

Kuti padzikoli pakhale mtendere weniweni m’pofunika boma limene lingaphunzitse anthu kukhala mwamtendere

Baibulo limapereka zifukwa ziwiri. Chifukwa choyamba n’chakuti anthu sanalengedwe kuti azitha kudzilamulira okha. Chachiwiri n’chakuti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo,” yemwe ndi Satana Mdyerekezi. N’chifukwa chake zimene anthu akhala akuchita kuti abweretse mtendere padziko lonse zalephereka.—Werengani Yeremiya 10:23; 1 Yohane 5:19.

Chinthu chinanso chimene chikuchititsa kuti padzikoli pasakhale mtendere weniweni n’chakuti anthu ndi odzikonda komanso adyera. Kuti padzikoli pakhale mtendere m’pofunika boma limodzi lolamulira dziko lonse, lomwe lingaphunzitse anthu kuti azikonda kuchita zinthu zabwino komanso kuti azikonda anthu anzawo.—Werengani Yesaya 32:17; 48:18, 22.

Ndani adzabweretsa mtendere padzikoli?

Mulungu yemwe ndi Wamphamvuyonse walonjeza kuti adzakhazikitsa boma limene lidzalamulire dziko lonse lapansi. Bomalo lidzathetsa maboma onse a anthu. (Danieli 2:44) Yesu, yemwe ndi Mwana wa Mulungu, adzalamulira monga Kalonga Wamtendere. Iye adzachotsa anthu onse ochita zoipa ndipo adzaphunzitsa anthu kukhala mwamtendere.—Werengani Yesaya 9:6, 7; 11:4, 9.

Panopa, Yesu wayamba kale kuphunzitsa anthu kukhala mwamtendere. Iye akuchita zimenezi potsogolera ntchito yophunzitsa anthu Baibulo imene otsatira ake akuchita padziko lonse lapansi. Posachedwapa, padzikoli padzakhala mtendere weniweni.—Werengani Yesaya 2:3, 4; 54:13.