Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZITSANI ANA ANU

Petulo ndi Hananiya Ananama, Kodi Tikuphunzirapo Chiyani?

Petulo ndi Hananiya Ananama, Kodi Tikuphunzirapo Chiyani?

Monga ukudziwira, kunama kumatanthauza kunena zinthu zimene ukudziwa kuti n’zabodza. Kodi iweyo unayamba wanama? * Ngakhale akuluakulu ena amene amakonda Mulungu ananamapo. Mwinanso ukudziwa munthu wina wotchulidwa m’Baibulo amene ananama. Dzina lake ndi Petulo ndipo anali mmodzi mwa atumwi a Yesu. Tiye tikambirane zimene zinachititsa kuti aname.

Yesu atamangidwa, anapita naye kunyumba kwa mkulu wansembe. Pa nthawiyi n’kuti nthawi itapitirira 12 koloko usiku. Petulo anafika kubwalo la nyumba ya mkulu wansembeyo ndipo anthu sanamuzindikire. Koma chifukwa cha kuwala kwa moto, mtsikana wantchito amene anatsegulira Petulo, anamuzindikira ndipo anati: “Inunso munali ndi Yesu.” Chifukwa cha mantha, Petulo anakana kuti amadziwa Yesu.

Baibulo limati kenako mtsikana wina anazindikiranso Petulo, ndipo anati: “Bambo awa anali limodzi ndi Yesu.” Koma Petulo anakananso. Patapita nthawi anthu ena anauzanso Petulo kuti: “Ndithu iwenso uli m’gulu la ophunzira ake.”

Petulo anayamba kuchita mantha, choncho ananama ponena kuti: “Munthu ameneyu ine sindikumudziwa ayi!” Kenako tambala analira. Yesu anayang’ana Petulo ndipo Petuloyo anakumbukira mawu amene Yesu anamuuza akuti: “Tambala asanalire, udzandikana katatu.” Petulo anadzimvera chisoni ndipo anayamba kulira. Iye anazindikira kuti walakwa kwambiri.

Kodi zinthu zoterezi zingakuchitikirenso iweyo?— Ungakhale uli kusukulu ndipo ungamve ana a sukulu anzako akunena za Mboni za Yehova. Iwo anganene kuti: “A mboni sachitira sailuti mbendera.” Wina anganene kuti: “Komanso samenyera nkhondo dziko lawo.” Ndipo mwina wina angati: “Anthu amenewa si Akhristu enieni chifukwa sakondwerera Khirisimasi.” Ndiyeno wina angakufunse kuti: “Paja iwenso ndiwe wa Mboni eti?” Kodi pamenepa ungatani?

 Uyenera kukonzekera kuti uzidziwiratu zomwe ungayankhe zimenezi zitakuchitikira. Petulo sanakonzekere, choncho anthu atamupanikiza, ananama. Komabe iye anazindikira kulakwa kwake n’kulapa, ndipo Mulungu anamukhululukira.

Wophunzira wina wa Yesu, dzina lake Hananiya, nayenso ananama. Koma Mulungu sanamukhululukire komanso sanakhululukire mkazi wake Safira. Iwo anachita kugwirizana kuti aname. Tiye tione chifukwa chake Mulungu sanawakhululukire.

Patatha masiku 10 kuchokera pamene Yesu anakwera kumwamba, anthu pafupifupi 3,000 anabatizidwa ku Yerusalemu. Ambiri mwa anthu amenewa anachokera kumadera akutali kudzachita nawo Chikondwerero cha Pasika. Atakhala ophunzira a Yesu, sanafune kubwerera msanga kwawo chifukwa ankafuna kuti aphunzire zambiri zokhudza Chikhristu. Choncho ophunzira ena a Yesu ankapereka ndalama zoti zithandizire anthuwa.

Hananiya ndi mkazi wake anagulitsa munda wawo kuti apereke ndalama zothandizira anthu amenewa. Hananiya anatenga ndalama za mundawu n’kupita nazo kwa atumwi n’kunena kuti zinali zonse zimene anagulitsira mundawo. Koma limenelitu linali bodza chifukwa iye anali atasunga ndalama zina. Mulungu anathandiza Petulo kudziwa za bodzali ndipo Petuloyo anauza Hananiya kuti: “Pamenepa sikuti wanamiza anthu ayi, koma Mulungu.” Nthawi yomweyo Hananiya anagwa pansi n’kumwalira. Patatha maola atatu, mkazi wake anafika. Iye sanadziwe zimene zinachitikira mwamuna wake ndipo nayenso anamana. Zitatere iyenso anagwa n’kufa.

Pamenepatu pali phunziro lalikulu kwa tonsefe. Kunama n’koipa. Komabe tonsefe nthawi zina timalakwitsa, makamaka tikakhala ana. Kodi si zosangalatsa kuti Yehova amakukonda ndipo adzakukhululukira ngati mmene anachitira ndi Petulo?— Komabe usaiwale kuti tiyenera kupewa bodza. Tikanama, tiyenera kupempha Mulungu kuti atikhululukire. Izi n’zimene Petulo anachita, ndipo Mulungu anamukhululukira. Ngati timayesetsa kupewa bodza, nafenso Mulungu adzatikhululukira titanama mwangozi.

^ ndime 3 Ngati mukuwerengera mwana nkhaniyi, mukapeza mzera muime kaye ndi kumulimbikitsa kuti anenepo maganizo ake.