Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Masoka Achilengedwe Achuluka Chonchi?

N’chifukwa Chiyani Masoka Achilengedwe Achuluka Chonchi?

MASIKU ano, tikungokhalira kumva za masoka achilengedwe, ndipo anthu ambiri akukhudzidwa ndi masoka osiyanasiyana kuposa kale lonse. Bungwe lina la ku Belgium lochita kafukufuku pa za masoka achilengedwe linanena kuti mu 2010 mokha, panachitika masoka achilengedwe okwana 373 ndipo anthu oposa 296,000 anafa pa masoka amenewa.

Komanso chiwerengero cha masoka achilengedwe chakwera kwambiri pa zaka zapitazi. Mwachitsanzo, kuyambira mu 1975 mpaka mu 1999, chaka chilichonse pankachitika masoka odziwika osakwana 300. Koma kuyambira m’chaka cha 2000 mpaka mu 2010, chiwerengerochi chinakwera kufika pa masoka pafupifupi 400 chaka chilichonse. Choncho n’kutheka kuti ndinu mmodzi wa anthu amene amadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani masoka achilengedwe achuluka kwambiri masiku ano?’

Nthawi zambiri anthu amanena kuti Mulungu ndi amene amachititsa masoka achilengedwe, koma zimenezi si zoona. Mulungu si amene amachititsa masoka achilengedwe amene akugwera anthu ambiri masiku ano. Komabe, Baibulo linalosera kuti masoka osiyanasiyana adzachitika m’nthawi yathu ino. Mwachitsanzo, pa Mateyu 24:7, 8, timawerenga mawu a Yesu akuti: “Kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana. Zonsezi ndi chiyambi cha masautso, ngati mmene zimayambira zowawa za pobereka.” Kodi n’chifukwa chiyani Yesu analosera zinthu zimenezi, ndipo zikutanthauza chiyani kwa ife?

Yesu, yemwe ndi Mwana wa Mulungu, ananena zimenezi poyankha funso lakuti: ‘Kodi chizindikiro cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?’ (Mateyu 24:3) Iye anafotokoza zinthu zosiyanasiyana zimene zidzachitike, kuphatikizapo masoka ngati amene angotchulidwa kumenewa. Kenako iye ananena mfundo yochititsa chidwi kwambiri, yakuti: “Mukadzaona zimenezi zikuchitika, mudzadziwe kuti ufumu wa Mulungu wayandikira.” (Luka 21:31) Choncho, masoka achilengedwe amene akuchitikawa ali ndi tanthauzo lapadera kwambiri kwa ife chifukwa akusonyeza kuti posachedwapa zinthu zisintha kwambiri.

Zimene Zikuchititsa Masoka Achilengedwe

Ngakhale zili choncho, anthu ambiri amafunsabe kuti, Ngati Mulungu si amene amachititsa masoka achilengedwe, ndani kapena n’chiyani chimawachititsa? Kuti timvetse yankho la funso limeneli tiyenera kuzindikira mfundo ya choonadi yotchulidwa m’Baibulo, yakuti: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Vesi limeneli likusonyezeratu kuti si Mulungu amene amayambitsa mavuto m’dzikoli, koma nthawi zambiri ndi mdani wake, yemwe ndi “woipayo” amene amatchulidwa m’Baibulo kuti “Mdyerekezi.”​—Chivumbulutso 12:9, 12.

Mdani wa Mulungu ameneyu ali ndi mtima wadyera ndipo amaona moyo wa munthu ngati chinthu chopanda ntchito. Popeza dziko lonse lili m’manja mwake, iye wachititsa kuti anthu akhale ndi mtima wofanana ndi wakewo. Zoonadi, Baibulo linkanena zimenezi pamene linalosera kuti ‘m’masiku otsiriza’ anthu “adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza.” (2 Timoteyo 3:1, 2) Choncho n’zosadabwitsa kuti Mdyerekezi wachititsa kuti anthu padziko lonse akhale ndi mtima umenewu komanso azichita makhalidwe ena oipa osalemekeza Mulungu. Iye amalimbikitsa anthu kuti azichita zinthu zosonyeza kudzikonda komanso mtima wadyera, zomwe nthawi zambiri zimaika moyo wa ena pangozi.

Kodi masiku ano dziko la anthu adyerali likuthandizira bwanji kuti masoka achilengedwe azichitika? Lipoti lina lokhudza masoka achilengedwe padziko lonse, limene bungwe la United Nations linatulutsa, linati: “Kawirikawiri anthu ambirimbiri akumakhala m’madera amene mumachitikachitika masoka achilengedwe, monga m’zigwa momwe mumasefukira madzi. Kuwonjezera apo, kusakazidwa kwa nkhalango ndiponso madambo kukuchititsa kuti mphamvu imene imateteza dzikoli ku zinthu zowononga ichepe. Vuto lalikulu kwambiri pa mavuto onsewa ndi lokhudza kusintha kwa nyengo ndi kukwera kwa madzi a m’nyanja, zomwe zikuchitika chifukwa cha kuwonjezereka kwa mpweya woipa . . . womwe umatuluka m’zinthu monga mafakitale.” Ngakhale kuti anthu amati zambiri mwa zinthu zotulutsa mpweya woipazi zimathandiza kuti chuma chiziyenda bwino, zoona zake n’zakuti zimenezi zimangosonyeza mtima wodzikonda ndiponso wadyera umene uli ponseponse m’dzikoli.

Choncho, akatswiri ambiri tsopano azindikira kuti zochita za anthu zowononga chilengedwe, n’zimene zikuthandizira kwambiri kuti masoka achilengedwe azichitika. Kunena zoona, Mdyerekezi akungogwiritsira ntchito anthu a m’dzikoli pofuna kukwaniritsa zolinga zake. Iye akufuna kubweretsa mavuto ochuluka zedi kwa ena komanso kuchititsa kuti masoka achilengedwe azichulukirachulukira.

Motero tikuona kuti masoka ambiri amachitika chifukwa choti anthu amachita zinthu zina mosasamala. Masoka ena achilengedwe amakhala oopsa kwambiri chifukwa cha dera limene achitikira. Ndipo m’madera ambiri padzikoli, zochita za anthu oipa n’zimene zimachititsa kuti masoka achilengedwe akhale oopsa kwambiri. Chinanso chimene chimachititsa kuti masokawa akhale oopsa kwambiri n’choti anthu ambirimbiri amakakamizika kukakhala m’madera amene mumachitika masokawo kawirikawiri. Anthuwo amakakamizika kukakhala m’madera amenewa chifukwa cha mavuto azachuma, omwe ndi ofala kwambiri m’dzikoli. Komabe, anthu ena amavutika ndi masoka achilengedwe osati chifukwa cha vuto la munthu winawake kapena chifukwa chosaganiza bwino, koma chifukwa choti “nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo.”​—Mlaliki 9:11.

Kodi mungatani kuti mupirire ngati mwakumana ndi tsoka lachilengedwe pa zifukwa zosiyanasiyana? Tsopano tikambirana zimene mungachite kuti musavutike kwambiri mukakumana ndi tsoka lachilengedwe.