Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Sakuona Zikuchitikazi?

Kodi Mulungu Sakuona Zikuchitikazi?

Kodi Mulungu Sakuona Zikuchitikazi?

September 11, 2001: Nthawi ya 8:46 m’mawa, ndege yaikulu yonyamula anthu inawomba imodzi mwa nyumba zosanja za ku World Trade Center ku New York City. Imeneyi inali imodzi mwa ndege zingapo zimene zigawenga zina zinalanda. Asanathe maola awiri izi zitachitika, anthu pafupifupi 3,000 anali atafa.

December 26, 2004

Chivomezi champhamvu zokwana 9.0, pa sikelo yoyezera mphamvu ya zivomezi, chinachitika m’nyanja ya Indian. Chivomezichi chinayambitsa mafunde aakulu amene anafika m’mayiko 11, kuphatikizapo a mu Africa omwe ali pamtunda wa makilomita 5,000 kuchokera komwe chivomezichi chinachitikira. Pa tsiku limodzi lokha anthu okwana 150,000 anafa kapena kusowa ndipo ena oposa 1 miliyoni nyumba zawo zinawonongeka.

August 1, 2009: Bambo wina wazaka 42 limodzi ndi mwana wake wazaka 5 anakwera bwato lothamanga kwambiri. Kenako bwatolo linawomba matabwa a padoko lina ndipo bamboyo anamwalirira pompo. Koma mwanayo anamwalira tsiku lotsatira. Mwachisoni, wachibale wa bamboyo anati: “Timaganiza kuti Mulungu achita zodabwitsa kuti mwana yekhayu apulumuke.”

Mukawerenga m’nyuzipepala nkhani zokhudza uchigawenga kapena masoka achilengedwe kapenanso mukakumana ndi tsoka linalake, kodi mumaganiza kuti mwina Mulungu sakuona zimene zikuchitikazi? Kapena kodi mumaganiza kuti watinyanyala? Zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi n’zokhazika mtima pansi. Taonani nkhani yotsatirayi.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

© Dieter Telemans/​Panos Pictures

PRAKASH SINGH/​AFP/​Getty Images

© Dieter Telemans/​Panos Pictures