Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ponena za Tsogolo la Anthu

Ponena za Tsogolo la Anthu

Zimene Tikuphunzira kwa Yesu

Ponena za Tsogolo la Anthu

Kodi Yesu analonjeza kuti anthu adzapita kumwamba?

Inde, analonjezadi zimenezi. Ndipo Yesu, amene analonjeza zimenezi, ataukitsidwa anapita kumwamba kukakhala ndi Atate wake. Koma asanaphedwe, anauza atumwi ake 11 okhulupirika kuti: “M’nyumba ya Atate wanga alimo malo ambiri okhalamo. . . . Ndikupita kukakukonzerani malo.” (Yohane 14:2) Komabe, anthu amene adzapite kumwamba ndi ochepa. Yesu ananena momveka bwino mfundo imeneyi pamene anauza ophunzira ake kuti: “Musaope, kagulu ka nkhosa inu, chifukwa Atate wanu wavomereza kukupatsani ufumu.”​—Luka 12:32.

Kodi “kagulu ka nkhosa” kakukatani kumwamba?

Atate akufuna kuti kagulu kameneka kakalamulire m’boma la kumwamba pamodzi ndi Yesu. Tikudziwa bwanji zimenezi? Ataukitsidwa, Yesu anauza mtumwi Yohane kuti anthu ena okhulupirika “adzalamulira dziko lapansi monga mafumu.” (Chivumbulutso 1:1; 5:9, 10) Umenewutu ndi uthenga wabwino chifukwa chimodzi mwa zinthu zimene anthu amafunitsitsa ndi boma labwino. Kodi boma lolamuliridwa ndi Yesu limeneli lidzachita zinthu zotani? Yesu anati: “Panthawi ya kukonzanso zinthu, pamene Mwana wa munthu adzakhala pa mpando wachifumu wa ulemerero, inu amene mwatsatira ine mudzakhalanso m’mipando yachifumu 12.” (Mateyo 19:28) Ulamuliro wa Yesu ndi otsatira ake ‘udzakonzanso zinthu,’ kapena kuti udzabwezeretsa moyo wabwino ndiponso mtendere umene Adamu ndi Hava anali nawo padzikoli asanachimwe.

Nanga Yesu ananena kuti anthu ena onse adzalandira madalitso otani?

Anthu analengedwa kuti azikhala padziko lapansi, koma Yesu analengedwa kuti azikhala kumwamba. (Salmo 115:16) N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Inu ndinu ochokera pansi pano; ine ndine wochokera kumwamba.” (Yohane 8:23) Iye anasonyeza kuti anthu adzakhala ndi moyo wabwino kwambiri padziko lino lapansi. Panthawi ina, iye anati: “Osangalala ali iwo amene ali ofatsa, popeza adzalandira dziko lapansi.” (Mateyo 5:5) Iye ananena zimenezi mogwirizana ndi mfundo yakuti: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka. Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”​—Salmo 37:11, 29.

Motero, pali anthu enanso amene adzalandire moyo wosatha kuwonjezera pa “kagulu ka nkhosa,” kamene kadzapite kumwamba. Yesu ananenanso zimene anthu onse padziko lapansi angayembekezere. Iye anati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.”​—Yohane 3:16.

Kodi Mulungu adzathetsa bwanji mavuto athu?

Yesu anatchula kuti zinthu ziwiri zomwe zimachititsa anthu kuvutika zidzachotsedwa. Iye anati: “Tsopano dziko ili likuweruzidwa; wolamulira wa dzikoli aponyedwa kunja tsopano.” (Yohane 12:31) Lembali likusonyeza kuti anthu oipa amene amachititsa anthu kuvutika adzaweruzidwa kenako n’kuwonongedwa. Ndiyeno, Satana adzaponyedwa kunja moti sadzathanso kusokoneza anthu.

Nanga bwanji anthu amene anamwalira asanaphunzire ndiponso kukhulupirira za Mulungu ndi Khristu? Yesu anauza munthu wochita zoipa amene anapachikidwa naye limodzi kuti: “Iwe udzakhala nane m’Paradaiso.” (Luka 23:43) Munthu ameneyo, komanso anthu ena ambiri, adzakhala ndi mwayi wophunzira za Mulungu, Yesu akadzamuukitsa m’paradaiso padziko lapansi. Iye akadzaphunzira, adzakhala ndi mwayi wokhala m’gulu la anthu ofatsa ndiponso olungama amene adzakhale ndi moyo wosatha padziko lapansi.​—Machitidwe 24:15.

Kuti mudziwe zambiri, onani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? pa mutu 3 ndi 7 *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 23]

“Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”​—Salmo 37:29