Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Yesu ankalankhula chinenero chanji?

Akatswiri a maphunziro samvana chimodzi pankhani ya chinenero chimene Yesu ankalankhula. Koma zikuoneka kuti Yesu ali padziko lapansi pano ankalankhula Chiheberi ndiponso Chiaramu. Yesu atafika mumzinda wa Nazarete ku Galileya n’kulowa m’sunagoge, anawerenga ulosi wa Yesaya, ndipo zikuoneka uti unali wolembedwa m’Chiheberi. Komabe Baibulo silinena chilichonse chosonyeza kuti Yesu anamasulira zimene ankawerengazo m’Chiaramu.​—Luka 4:16-21.

Ponena za zinenero za ku Palestina za m’nthawi ya Yesu, pulofesa G. Ernest Wright anati: “Zikuoneka kuti panthawiyo zinenero zotchuka zinali Chigiriki ndi Chiaramu. . . . Asilikali ndiponso akuluakulu achiroma ankalankhulana m’Chilatini, koma Ayuda ambiri ankalankhulana Chiheberi cha panthawi imeneyo.” Motero, n’zosadabwitsa kuti chikwangwani chimene Pilato anaika pa mtengo wozunzikirapo umene anapachikapo Yesu, analembapo zinenero zitatu. Zinenerozi ndi Chiheberi, Chilatini ndi Chigiriki.​—Yohane 19:20.

Munthu wina dzina lake Alan Millard analemba m’buku lake kuti: “N’zosakayikitsa kuti pantchito yawo ya tsiku ndi tsiku, akuluakulu aboma achiroma ankalankhulana m’Chigiriki ndipo n’kutheka kuti Yesu ankalankhula Chigiriki pa mlandu wake umene Pilato ankaweruza.” (Discoveries From the Time of Jesus) Ngakhale kuti Baibulo silinena kuti Yesu ankalankhula Chigiriki, n’zochititsa chidwi kuti nkhaniyo siinenanso kuti pamlanduwo panali munthu aliyense womasulira.​—Yohane 18:28-40.

Pulofesa Wright uja anati: “N’zovuta kunena motsimikiza kuti [Yesu] ankalankhula Chigiriki kapena Chilatini. Koma n’zosakayikitsa kuti nthawi zambiri ankagwiritsira ntchito Chiaramu kapena Chiheberi pantchito yake yophunzitsa anthu. Chihebericho n’chimene anthu ambiri ankalankhula panthawiyo, ndipo chinali chosakanikirana kwambiri ndi Chiaramu.”​—Biblical Archaeology, 1962, tsamba 243.

Kodi miyala ya kachisi wa ku Yerusalemu inali yaikulu motani?

Polankhula ndi Yesu, wophunzira wake anamulozera kachisi wa ku Yerusalemu n’kunena kuti: “Mphunzitsi, taonani mmene miyala ndi nyumbazi zikuonekera!” (Maliko 13:1) Kodi ina mwa miyala imeneyi inali yaikulu motani?

Mmene Yesu amafika padziko pano n’kuti Mfumu Herode atakulitsa malo amene anamangapo kachisi mowirikiza kawiri kuyerekezera ndi mmene analili m’nthawi ya Solomo. Masiku amenewo, malowa anali aakulu kwambiri kuposa malo ena alionse omangapo zinthu. Anali aakulu mamita 480 m’litali ndiponso mamita 280 m’lifupi. Akuti ina mwa miyala yake inali yaikulu mamita 11 m’litali, mamita asanu m’lifupi, ndiponso mamita atatu kupita m’mwamba. Miyala ingapo yotereyi inali yolemera matani oposa 50 mwala umodzi. Panalinso wina wolemera matani pafupifupi 400 ndipo katswiri wina wa mbiri yakale anati, “pa miyala yonse ya panthawiyo panalibenso wina waukulu kuposa umenewu.”

Poyankha wophunzira wake uja, Yesu anati: “Kodi ukuona nyumba zapamwamba zimenezi? Pano sipadzatsala mwala uliwonse pamwamba pa unzake umene sudzagwetsedwa.” (Maliko 13:2) Miyala yambiri ikuluikulu idakalipo ndipo ili pa malo amene asilikali achiroma anaigubuduzira m’chaka cha 70 C.E.

[Chithunzi patsamba 26]

Miyala ya Kachisi wa ku Yerusalemu Imene Anaigubuduza