Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyandikira kwa Mulungu Ndi Kwabwino

Kuyandikira kwa Mulungu Ndi Kwabwino

MUNTHUNE nditangokwanitsa zaka 9 ndinasiya kukula. Panopa ndili ndi zaka 43 ndipo ndine wamfupi mita imodzi yokha. Makolo anga atazindikira vuto langali ankandiuza kuti ndizigwira ntchito mwakhama n’cholinga choti ndisamaganizire kwambiri maonekedwe anga. Choncho ndinayamba kugulitsa zipatso ndipo ndinkaziyala mwaluso kuti zizioneka bwino. Izi zinkachititsa chidwi anthu ambiri moti ankabwera kudzagula.

Koma sikuti vuto langa linatheratu. Ndimavutikabe ndi zinthu zing’onozing’ono. Mwachitsanzo, m’masitolo ambiri sindifikira pakauntala. Zikuoneka kuti anthu akamamanga zinthu amangoganizira anthu aatali osati amsinkhu wanga. Poyamba ndinkadzimvera chisoni kwambiri koma ndinasintha maganizowa nditakwanitsa zaka 14.

Tsiku lina azimayi awiri a Mboni anabwera kudzagula zipatso ndipo kenako anayamba kundiphunzitsa Baibulo. Ndinazindikira kuti kudziwa Yehova komanso cholinga chake n’kofunika kwambiri kuposa kuganizira za kufupika kwanga. Mfundo imeneyi inandithandiza kwabasi. Ndinkakonda kwambiri lemba la Salimo 73:28. Mbali yoyamba ya vesili imanena kuti: “Kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino.”

Mwadzidzidzi, banja lathu linasamuka ku Côte d’Ivoire kupita ku Burkina Faso ndipo moyo wanga unasintha kwambiri. Tisanasamuke, anthu anazolowera kundiona ndikugulitsa zipatso. Koma ku Burkina Faso anthu ambiri ankandidabwa n’kumangondiyang’anitsitsa. Izi zinachititsa kuti ndizingodzitsekera m’nyumba kwa milungu ingapo. Kenako ndinakumbukira mmene ndinkamvera nditangodziwa kumene za Yehova. Choncho ndinalemba kalata ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ndipo ananditumizira mmishonale wina dzina lake Nani kuti apitirize kundiphunzitsa. Iye ankabwera pa njinga yamoto ndipo ndinkagwirizana naye.

Misewu ya kumene tinkakhala inali yovuta ndipo nthawi ya dzinja inkakhala matope okhaokha. Nani ankagwa ndi njinga yakeyo maulendo ambirimbiri koma ankabwerabe kudzandiphunzitsa. Tsiku lina anandipempha kuti ndipite naye ku misonkhano. Apa ndinadziwa kuti tsopano ndiyenera kutuluka m’nyumba ngakhale kuti anthu azindiyang’anitsitsa. Ndinkadanso nkhawa poganiza kuti iye azivutika kwambiri kuyendetsa njingayo akandikweza. Koma ndinavomerabe pokumbukira mbali yachiwiri ya lemba londisangalatsa lija, imene imati: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa ndiye pothawirapo panga.”

Nthawi zina ine ndi Nani tinkagweranso m’matope koma sitinkadandaula chifukwa tinkakonda kwambiri kusonkhana. Popita ku Nyumba ya Ufumu anthu ankandiyang’anitsitsa kwambiri koma ndikafika abale ndi alongo ankandilandira bwino. Patangopita miyezi 9, ndinabatizidwa.

Mbali yachitatu ya lemba limene ndimalikonda lija imati: “Ndilengeze za ntchito zanu zonse.” Ndinkadziwa kuti ndizivutika kwambiri kulalikira. Ndimakumbukira zimene zinachitika nditapita kukalalikira tsiku loyamba. Ana ndi achikulire omwe ankandiyang’anitsitsa, kunditsatira ndiponso ankayerekezera mmene ndimayendera. Zinkandiwawa kwambiri koma ndinkalalikirabe pokumbukira kuti nawonso ayenera kuthandizidwa kuti akalowe m’Paradaiso.

Ndinagula kanjinga kamatayala atatu kopalasa ndi manja kuti ndisamavutike polalikira. Tikafika pamtunda, munthu amene ndinkalalikira naye ankandikankha ndipo tikafika potsetsereka ankakwera nawo njingayo. N’zoona kuti poyamba ntchito yolalikira inkandivuta koma kenako ndinayamba kuikonda kwambiri. Pofika mu 1998, ndinalembetsa upainiya wokhazikika.

Ndinkaphunzitsa anthu ambiri ndipo anthu 4 anabatizidwa. Ndinasangalala kwambiri kuti mng’ono wanga anayambanso kutumikira Yehova. Ndikamva mmene anthu ena akusinthira chifukwa chophunzira Baibulo, ndimasangalala kwambiri ndipo zimandilimbikitsa. Mwachitsanzo, tsiku lina ndikudwala malungo, ndinalandira kalata yochokera kwa mnyamata wina amene ankakhala ku Côte d’Ivoire. Ndinayamba kuphunzira naye pa nthawi imene anali kuyunivesite ndipo kenako ndinasiyira m’bale wina kuti aziphunzira naye. Kenako anasamukira ku Côte d’Ivoire ndipo ndinasangalala kumva kuti anali wofalitsa wosabatizidwa.

Bungwe lina lothandiza anthu olumala linayamba kundiphunzitsa kusoka. Koma mphunzitsi wina ataona kuti ndine wakhama anaganiza zondiphunzitsa kapangidwe ka sopo. Bungweli linandiphunzitsadi ndipo anthu ambiri amakonda sopo amene ndimapanga moti amandipezera makasitomala ena. Panopa ndili ndi njinga yamoto yamatayala atatu imene ndimagwiritsa ntchito pokapereka sopoyu kwa anthu.

Koma mu 2004, msana wanga unayamba kupweteka kwambiri moti ndinaona kuti ndi bwino kusiya upainiya. Koma ndimayesetsabe kulalikira mwakhama.

Anthu amanena kuti ndimakonda kumwetulira. Munthune ndimasangalaladi chifukwa chakuti kuyandikira kwa Mulungu ndi kwabwino.—Yofotokozedwa ndi Sarah Maiga.