Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzilemekeza Anthu Achikulire

Muzilemekeza Anthu Achikulire

“Munthu wachikulire uzim’patsa ulemu.”—LEV. 19:32.

1. Kodi anthu akukumana ndi zotani masiku ano?

CHOLINGA cha Yehova sichinali choti anthu azivutika ndi ukalamba. Iye ankafuna kuti anthu azisangalala m’Paradaiso ali ndi thanzi labwino. Koma panopa “chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zowawa.” (Aroma 8:22) Kodi mukuganiza kuti Yehova amamva bwanji akamaona anthu akuvutika chifukwa cha zotsatira za uchimo? N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri sasamala okalamba pa nthawi imene amafunikira kwambiri thandizo.—Sal. 39:5; 2 Tim. 3:3.

2. N’chifukwa chiyani Akhristu amalemekeza kwambiri achikulire?

2 Anthu a Yehova amasangalala kukhala ndi achikulire mumpingo. Timapindula kwambiri chifukwa cha nzeru zawo komanso chikhulupiriro chawo. N’kutheka kuti ena mwa achikulirewa ndi achibale athu. Koma kaya ndi achibale athu kapena ayi, tiyenera kuwakonda ndiponso kuwathandiza. (Agal. 6:10; 1 Pet. 1:22) Kudziwa mmene Yehova amaonera achikulire kungatithandize kwambiri. Tsopano tiyeni tikambirane zimenezi ndiponso udindo umene achibale komanso mpingo uli nawo powasamalira.

“MUSANDITAYE”

3, 4. (a) Kodi wolemba Salimo 71 anapempha chiyani kwa Yehova? (b) Kodi Akhristu achikulire angapemphe chiyani kwa Mulungu?

3 Munthu amene analemba Salimo 71:9 anachonderera  Mulungu kuti: “Musanditaye nthawi ya ukalamba wanga. Musandisiye pa nthawi imene mphamvu zanga zikutha.” Zikuoneka kuti munthu amene analemba salimoli ndi amene analembanso Salimo 70, lomwe lili ndi timawu tapamwamba takuti: “Salimo la Davide.” Choncho Davide ayenera kuti ndi amene ananena mawu a pa Salimo 71:9 amenewa. Iye anatumikira Mulungu kuyambira ali wachinyamata mpaka kukalamba ndipo Yehova anamugwiritsa ntchito kuchita zinthu zikuluzikulu. (1 Sam. 17:33-37, 50; 1 Maf. 2:1-3, 10) Ngakhale zili choncho, Davide ankapempha Mulungu kuti apitirize kumuthandiza.—Werengani Salimo 71:17, 18.

4 Mofanana ndi Davide, masiku ano pali anthu amene amayesetsabe kutamanda Mulungu ngakhale kuti akalamba ndipo ali ‘m’masiku oipa.’ (Mlal. 12:1-7) Mwina iwo sangachite zambiri mu utumiki kapena pa zinthu zina ngati mmene ankachitira kale. Koma akhoza kupempha Yehova kuti aziwakondabe ndiponso kuwasamalira. Achikulire okhulupirikawa sayenera kukayikira kuti Mulungu ayankha mapemphero awo. Tikutero chifukwa chakuti mapemphero awowo akufanana ndi mapemphero a Davide omwe tikuwapeza m’Baibulo.

5. Kodi Yehova amaona bwanji achikulire okhulupirika?

5 Malemba amasonyeza kuti Yehova amaona kuti achikulire okhulupirika ndi amtengo wapatali kwambiri ndipo amafuna kuti tiziwalemekeza. (Sal. 22:24-26; Miy. 16:31; 20:29) Lemba la Levitiko 19:32 limati: “Anthu aimvi uziwagwadira, munthu wachikulire uzim’patsa ulemu ndipo uziopa Mulungu wako. Ine ndine Yehova.” Pa nthawi imene mawuwa analembedwa, kulemekeza achikulire kunali kofunika kwambiri ndipo ndi mmene zililinso masiku ano. Koma kodi ndani ali ndi udindo wowasamalira?

UDINDO WA ACHIBALE

6. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pa nkhani yosamalira makolo?

6 Mawu a Mulungu amati: “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.” (Eks. 20:12; Aef. 6:2) Yesu anatsindika mfundo imeneyi podzudzula Afarisi ndi alembi amene ankakana kusamalira makolo awo. (Maliko 7:5, 10-13) Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani imeneyi. Mwachitsanzo, iye atatsala pang’ono kumwalira pamtengo wozunzikirapo, anapereka mayi ake m’manja mwa Yohane kuti aziwasamalira. Zikuoneka kuti pa nthawiyi amayi akewo anali amasiye.—Yoh. 19:26, 27.

7. (a) Kodi mtumwi Paulo ananena chiyani pa nkhani yosamalira makolo? (b) Kodi Paulo ankakamba nkhani yotani ponena mawu amenewa?

7 Mtumwi Paulo analemba kuti atumiki a Mulungu ayenera kusamalira anthu a m’banja lawo. (Werengani 1 Timoteyo 5:4, 8, 16.) Kodi Paulo ankakamba nkhani yotani ponena mawu amenewa kwa Timoteyo? Iye ankanena za anthu amene anali oyenera komanso osayenera kulandira thandizo la ndalama kuchokera kumpingo. Paulo anafotokoza momveka bwino kuti ana, zidzukulu komanso achibale ena okhulupirira ndi amene ali ndi udindo waukulu wosamalira akazi amasiye omwe anali achikulire. Izi zinathandiza kuti mpingo usamavutike kufufuza ndalama zosamalira amasiye. Masiku anonso, Akhristu amasonyeza kuti ndi “odzipereka kwa Mulungu” posamalira achibale awo osowa.

8. N’chifukwa chiyani Baibulo silipereka malangizo achindunji oti tizitsatira posamalira makolo okalamba?

8 Mwachidule tinganene kuti Akhristu omwe ali ndi makolo achikulire ali ndi udindo wowasamalira. M’nkhaniyi Paulo ankanena za ‘achibale okhulupirira.’ Komabe ngati munthu ali ndi makolo omwe si atumiki a Mulungu, ayenerabe kuwasamalira. Ana  amasamalira makolo awo m’njira zosiyanasiyana malinga ndi mmene zinthu zilili pa moyo wawo. Mwachitsanzo, anthu akhoza kusiyana zinthu zimene akufunika, khalidwe lawo komanso thanzi lawo. Achikulire ena ali ndi ana ambiri, koma ena ali ndi mmodzi yekha. Ena angalandire thandizo lochokera ku boma koma ena sangalandire. Zinthu zimene anthu achikulirewo amakonda zimasiyanasiyananso. Choncho si bwino kutsutsa zimene anthu ena akuchita poyesetsa kusamalira achibale awo achikulire. Ndipotu Yehova angadalitse zilizonse zimene munthu wasankha mogwirizana ndi mfundo za m’Malemba. Iye wakhala akuchita zimenezi kuyambira m’nthawi ya Mose.—Num. 11:23.

9-11. (a) Kodi ena angakumane ndi mavuto otani? (Onani chithunzi patsamba 20.) (b) N’chifukwa chiyani anthu sayenera kufulumira kusiya utumiki wawo kuti akasamalire makolo? Perekani chitsanzo.

9 Ngati ana akukhala kutali ndi makolo awo okalamba, zingavute kuwasamalira. Mwana angafunike kupita kukaona makolo ake ngati akudwala, ngati anagwa n’kuthyoka fupa kapena ngati akumana ndi mavuto ena. Ndiyeno mwina makolowo angafunike thandizo kwa kanthawi kochepa kapena kwa nthawi yaitali. *

10 Abale ndi alongo ena amene ali mu utumiki wa nthawi zonse ndipo akutumikira kutali ndi kwawo, angavutike kusankha zochita pa nkhani imeneyi. Anthu amene akutumikira pa Beteli, amishonale komanso oyang’anira oyendayenda amaona kuti utumiki wawo ndi wamtengo wapatali komanso ndi madalitso ochokera kwa Yehova. Komabe, ngati makolo awo akudwala, angafulumire kuganiza kuti, ‘Basi, tiyenera kusiya utumikiwu n’kubwerera kunyumba kuti tikawasamalire.’ Koma zingakhale bwino kupempherera nkhani imeneyi n’kuganizira zimene makolowo angafunike komanso zimene angakonde. Tisafulumire kuganiza zosiya utumiki chifukwa mwina sizingafunike kutero. N’kutheka kuti matendawo sangatenge nthawi yaitali komanso mwina ena mumpingo wa makolowo angathandize.—Miy. 21:5.

11 Taganizirani chitsanzo cha abale awiri amene ankatumikira kutali ndi kwawo. Wamng’ono anali mmishonale ku South America ndipo wamkulu ankatumikira kulikulu ku Brooklyn, mumzinda wa New York. Makolo a abale amenewa anali achikulire ndipo ankafunikira thandizo. Abalewa limodzi ndi akazi awo anapita kukaona makolo awowo ku Asia kuti adziwe mmene angawathandizire. Patapita nthawi, m’bale amene ankatumikira ku South America uja limodzi ndi mkazi wake anayamba kuganiza zosiya utumiki wawo kuti abwerere kwawo. Kenako wogwirizanitsa ntchito za bungwe la akulu wa mpingo wa makolo akewo anamuimbira foni. Akuluwo anali atakambirana nkhaniyi ndipo ankafuna kuti amishonalewo apitirize utumiki wawo. Iwo ankayamikira kwambiri utumiki wa amishonalewo ndipo ankafunitsitsa kuchita zonse zimene akanatha kuti athandize kusamalira makolowo. Anthu onse m’banjamo anayamikira kwambiri zimene akuluwo anachita.

12. Kodi Akhristu ayenera kuganizira mfundo iti posamalira makolo awo achikulire?

12 Kaya achibale akufuna kuchita zotani posamalira makolo okalamba, aliyense ayenera kuonetsetsa kuti zimene akuchitazo zilemekeze dzina la Mulungu. Tisakhale ngati atsogoleri achipembedzo a nthawi ya Yesu. (Mat. 15:3-6) Nthawi zonse tizipewa kuchita zinthu zimene zinganyozetse Yehova kapena mpingo.—2 Akor. 6:3.

 UDINDO WA MPINGO

13, 14. N’chifukwa chiyani tinganene kuti mpingo uli ndi udindo wochokera m’Malemba wothandiza achikulire?

13 Si aliyense amene angathandize atumiki a nthawi zonse m’njira imene tafotokozayi. Koma malinga ndi zimene zinachitika m’nthawi ya atumwi, mpingo ulinso ndi udindo wosamalira Akhristu achikulire okhulupirika. Baibulo limanena kuti mumpingo wa ku Yerusalemu ‘munalibe ngakhale mmodzi wosowa.’ Apa sikuti onse anali opeza bwino. Zikuoneka kuti ena anali osauka koma ndalama zimene mpingo unkapeza “anali kuzigawa kwa aliyense malinga ndi zosowa zake.” (Mac. 4:34, 35) Koma kenako mumpingowu munabuka vuto lina. Zinamveka kuti ‘akazi ena amasiye ankanyalanyazidwa pa kagawidwe ka chakudya cha tsiku ndi tsiku.’ Choncho atumwi anauza abale kuti afufuze amuna a mbiri yabwino kuti ayang’anire ntchitoyi n’kuonetsetsa kuti akazi amasiye onse akuthandizidwa moyenera komanso mosakondera. (Mac. 6:1-5) N’zoona kuti zimenezi zinangochitika pa nthawi yochepa n’cholinga chothandiza anthu amene anakhala Akhristu pa Pentekosite mu 33 C.E. Akhristu amenewa anakhalabe ku Yerusalemu kuti aphunzire zambiri. Komabe zimene atumwiwa anachita zikusonyeza kuti mpingo uli ndi udindo wosamalira Akhristu ovutika.

14 Paja tanena kale kuti Paulo anafotokozera Timoteyo mmene angadziwire akazi amasiye amene akuyenera kulandira thandizo mumpingo ndi amene sakuyenera. (1 Tim. 5:3-16) Nayenso Yakobo anauziridwa kulemba kuti Akhristu ali ndi udindo wosamalira ana amasiye, akazi amasiye komanso anthu ena amene ali m’masautso. (Yak. 1:27; 2:15-17) Mtumwi Yohane ananenanso kuti: “Aliyense amene ali ndi zinthu zofunika pa moyo, n’kuona m’bale wake zikumusowa, koma osamusonyeza m’bale wakeyo chifundo chachikulu, kodi munthu ameneyu amakonda Mulungu?” (1 Yoh. 3:17) Ngati Mkhristu aliyense ali ndi udindo wothandiza anthu osowa ndiye kuti mpingo nawonso uyenera kuwathandiza.

Kodi mpingo ungathandize bwanji pakachitika ngozi? (Onani ndime 15, 16)

15. Fotokozani zinthu zina zimene anthu ayenera kuganizira pothandiza achikulire.

15 M’mayiko ena, boma limathandiza okalamba mwina powapatsa ndalama akapuma pa ntchito kapena kuwasamalira m’njira zina. (Aroma 13:6) Koma m’mayiko ena izi sizichitika. Choncho zimene achibale komanso mpingo ungachite pothandiza achikulirewa zimakhala zosiyanasiyana.  Koma ngati Akhristu ena amakhala kutali ndi makolo awo achikulire, kuwasamalira kungakhale kovuta. Akhristu oterewa angachite bwino kumalankhulana ndi akulu a mumpingo wa makolo awo kuti adziwe zoyenera kuchita. Mwachitsanzo, akuluwo angathandize makolowo kuti adziwe zoyenera kuchita kuti alandire chithandizo chaboma ngati chilipo. Angadziwitsenso anawo ngati makolo awo ali ndi ngongole zina kapena ngati sakulandira bwinobwino chithandizo chakuchipatala. Zoterezi zimathandiza kuti apeze njira zothetsera mavuto ena kuti asafike poipa. Anthu amene amaonetsetsa zimene zikuchitikira achikulire n’kudziwitsa ana awo, amathandizanso kuti anawo asamadere nkhawa kwambiri za makolo awo.

16. Kodi Akhristu ena amachita zotani posamalira achikulire?

16 Abale ndi alongo ena amakonda kwambiri anthu achikulire moti amadzipereka kuti aziwathandiza pa vuto lililonse limene angakumane nalo. Amangowatenga ngati makolo awo ndipo nthawi zina amasinthanasinthana ndi Akhristu ena powasamalira. Iwo amadziwa kuti sangakwanitse kuchita utumiki wa nthawi zonse, choncho amathandiza makolowo pofuna kuti ana awo apitirize utumiki umene akuchita. Abale ndi alongo amene amachita zimenezi tiyenera kuwayamikira kwambiri. Koma ngakhale zili choncho, ana a achikulirewo amakhalabe ndi udindo wowasamalira.

MUZILEMEKEZA ACHIKULIRE POWALIMBIKITSA

17, 18. Kodi ndi zinthu zinanso ziti zofunika posamalira achikulire?

17 Onse amene amasamalira achikulire ayenera kuchita zimenezi mosangalala. Ngati inuyo mukusamalira achikulire, yesetsani kuti achikulirewo azidziona kuti ndi ofunika. Nthawi zina achikulire angataye mtima kapena kukhala ndi nkhawa chifukwa cha ukalamba. Choncho muyenera kuyesetsa kulemekeza ndi kulimbikitsa abale ndi alongo achikulirewa. Ena atumikira Mulungu modzipereka kwa zaka zambiri ndipo tiyenera kuwayamikira. Yehova komanso Akhristu anzawo sadzaiwala utumiki umene achita.—Werengani Malaki 3:16; Aheberi 6:10.

18 Achikulirewo angaiwale mavuto awo ngati nthawi zina iwowo komanso amene akuwasamalira amachita nthabwala. (Mlal. 3:1, 4) Achikulire ambiri safuna kuti azivutitsa amene akuwasamalira. Amadziwa kuti akakhala ovuta anthu sangafune kuwasamalira kapena kuwachezera. Nthawi zambiri anthu akapita kukachezera munthu wachikulire amanena kuti, “Ndinapita kukalimbikitsa agogo aja, koma iwowo ndi amene andilimbikitsa.”—Miy. 15:13; 17:22.

19. Kodi achinyamata komanso achikulire akuyembekezera chiyani m’tsogolo?

19 Tikulakalaka mavuto obwera chifukwa cha uchimowa atatha. Koma panopa atumiki a Mulungu ayenera kupitiriza kuyembekezera madalitso osatha m’tsogolomu. Tikudziwa kuti kukhulupirira malonjezo a Mulungu kumatithandiza kupirira tikamakumana ndi mavuto. N’chifukwa chake “sitikubwerera m’mbuyo. Koma ngakhale munthu wathu wakunja akutha, ndithudi munthu wathu wamkati akukhalitsidwanso watsopano tsiku ndi tsiku.” (2 Akor. 4:16-18; Aheb. 6:18, 19) Koma kodi kuwonjezera pa kukhulupirira kwambiri malonjezo a Mulungu, ndi zinthu zina ziti zimene tingachite posamalira achikulire? Nkhani yotsatira tidzayankha funso limeneli.

^ ndime 9 M’nkhani yotsatira tidzakambirana zinthu zina zimene ana angachite posamalira makolo awo achikulire.